Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 45

Aoloka Mtsinje Wa Yorodano

Aoloka Mtsinje Wa Yorodano

ONA! Aisiraeli aoloka mtsinje wa Yorodano! Nanga madzi ali kuti? Popeza kuti mvula imagwa kwambili nthawi imeneyi, mtsinje unali wodzala, koma tsopano mulibe madzi! Ndipo Aisiraeli ayenda pouma monga mmene zinalili pamene anaoloka Nyanja Yofiila! Nanga madzi onse aja ayenda kuti? Tiye tione.

Pamene nthawi ifika yakuti Aisiraeli aoloke mtsinje wa Yorodano, Yehova alamula Yoswa kuti auze anthu kuti: ‘Ansembe adzanyamula likasa la cipangano ndi kukhala kutsogolo, koma ife tidzawatsatila kumbuyo. Ndipo io akangoponda mapazi ao mu mtsinje wa Yorodano, madzi adzaleka kuyenda.’

Conco ansembe anyamula likasa la cipangano, ndi kukhala kutsogolo kwa anthu. Pamene afika pa Yorodano, ansembe aponda m’madzi. Pamtsinje apa m’patali ndipo madzi ake athamanga kwambili. Koma pamene ansembe apondamo, madzi aleka kuyenda! Zimenezi n’zodabwitsa! Cakumene mtsinje ucokela, Yehova waimitsa madzi kukhala damu. Ndipo posapita nthawi, madzi onse auma mu mtsinje.

Ansembe amene anyamula likasa la cipangano ayenda mpaka pakati pa mtsinje wouma umenewu. Kodi waaona pacithunzi-thunzi apa? Iwo aimilila pamenepo mpaka Aisiraeli onse aoloke mtsinje wa Yorodano pouma.

Pamene onse atsiliza kuoloka, Yehova alamula Yoswa kuti auze amuna amphamvu 12 kuti: ‘Pitani mumtsinje pamene paimilila ansembe amene anyamula likasa la cipangano. Mutenge miyala 12, ndipo muiike kumene mudzagona lelo usiku. Ndiyeno mtsogolo ana anu akakufunsani za miyala imeneyi, mukawauze kuti madzi a mumtsinje wa Yorodano anauma pamene likasa la Yehova la cipangano linali kuoloka mtsinjewo. Miyala iyi idzakukumbutsani za cozizwitsa cimeneci.’ Naye Yoswa atenga miyala ina 12 ndi kuiika pamalo pamene paimilila ansembe mu pamtsinjepo.

Potsilizila pake, Yoswa auza ansembe amene anyamula likasa la cipangano kuti: ‘Cokani mumtsinje wa Yorodano.’ Pamene io angocokamo, madzi ayambanso kuyenda.

Yoswa 3:1-17; 4:1-18.