Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 47

Mbala mu Israyeli

Mbala mu Israyeli

ONANI chimene chikukwiriridwa ndi mwamuna’yu m’hema mwake! Mwainjiro wokongola, mkute wa golidi ndi timiyala ta siliva. Iye anazitenga m’Yeriko. Koma kodi paja zinthu za m’Yeriko anati zichitidwenji? Kodi mukukumbukira?

Izo zinayenera kuonongedwa, golidi ndi siliva n’kukasungidwa mosungira chuma m’chihema cha Yehova. Anthu’wa anyozatu Mulungu. Aba za Mulungu. Dzina la munthu’yu ndiro Akani, ndipo ali nayewo ndiwo ena a m’banja lake. Tiyeni tione zimene zikuchitika.

Akani ataba zinthu’zi, Yoswa akutumiza amuna ena kukamenyana ndi mzinda wa Ai. Koma akugonjetsedwa m’nkondo. Ena akuphedwa, otsala’wo nathawa. Yoswa ali n’chisoni kwambiri. Akugona chafufumimba napemphera kwa Yehova: ‘Mwaloleranji izi kutichitikira?’

Yehova akuyankha kuti: ‘Nyamuka! Israyeli wachimwa. Iwo atenga zinthu zoyenera kuonongedwa kapena kuperekedwa ku chihema cha Yehova. Aba mwiinjiro wokongola naubisa. Sindidzakudalitsani kufikira mutauononga, ndi wotenga zinthu’zi.’ Yehova akuti adzasonyeza Yoswa munthu woipa’yu.

Chotero Yoswa akusonkhanitsa anthu onse, Yehova nasonyeza Akani woipa’yo. Akani akuti: ‘Ndachimwa. Ndinaona mwiinjiro wokongola, ndi mkute wa golidi ndi timiyala ta siliva. Ndinazifuna kwambiri kwakuti ndinazitenga. Mudzazipeza zitakwiriridwa m’hema wanga.’

Zitapezeka zinthu’zi ndi kuperekedwa kwa Yoswa, akuti kwa Akani: ‘Watibvutitsiranji? Tsopano Yehova adzabvutitsa iwe!’ Pompo anthu onse anapha Akani ndi banja lake mwa kuwaponya miyala. Kodi izi sizikusonyeza kuti tisamatenga zinthu zosakhala zathu?

Pambuyo pake Israyeli akupita ku nkhondo kukamenyana’nso ndi Ai. Pa nthawi ino Yehova akuthandiza anthu ake napambana.