Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 51

Rute ndi Naomi

Rute ndi Naomi

M’BAIBULO muli bukhu lochedwa Rute. Iro n’nkhani yonena za banja lina limene linakhalako m’nthawi imene Israyeli anali ndi oweruza. Rute ndi mtsikana wa ku dziko la Moabu; sindiye wa mtundu wa Mulungu wa Israyeli. Koma atamva za Mulungu woona Yehova, akufikira pa kum’konda kwambiri. Naomi ndi mkazi wokalamba amene anathandiza Rute kuphunzira za Yehova.

Naomi ndi mkazi Wachiisrayeli. Iye ndi mwamuna wake ndi ana amuna awiri anasamukira ku dziko la Moabu kale pamene munali kusowa chakudya mu Israyeli. Ndiyeno tsiku lina mwamuna wa Naomi akufa. Kenako ana amuna a Naomi akukwatira akazi Achimoabu Rute ndi Oripa. Koma patapita zaka 10, ana awiri a Naomi’wo akufa. Ha, ndi achisoni chotani nanga m’mene Naomi ndi atsikana awiri’wo analiri! Kodi Naomi akanachitanji tsopano?

Tsiku lina Naomi akulinganiza za kuyenda ulendo wautali wobwerera kwa anthu ake. Rute ndi Oripa akufuna kukhala nayebe, ndipo chotero akumka naye. Koma atayenda kwa kanthawi, Naomi akutembenukira kwa atsikana’wo nati: ‘Bwererani kwanu ndi kukhala ndi amai anu.’

Naomi akuwapsyompsyona kutsazikana nawo. Pamenepo iwo akuyamba kulira, chifukwa chakuti amakonda kwambiri Naomi. Iwo akuti: ‘Ai! Tidzamka nanu kwa anthu akwanu.’ Koma Naomi akuyankha kuti: ‘Bwererani, ana anga. Zikakukhalirani bwino muli kwanu.’ Chotero Oripa akubwerera kwao. Koma Rute akukana kupita.

Naomi akutembenukira kwa iye nati: ‘Oripa wapita. Nawe’nso muka kwanu limodzi naye.’ Koma Rute akuyankha kuti: ‘Musayese kundichititsa kukusiyani! Ndiloleni ndimke nanu. Kumene mupita ndidzapita ine’nso, ndi kumene mudzakhala ndidzakhala ine’nso. Anthu akwanu adzakhala anthu akwathu, ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga. Kumene mudzafera ndidzafera ine’nso.’ Atatero, Naomi sakum’pangitsa’nso kumka kwao.

Potsirizira pake akazi awiri’wo akufika ku Israyeli. Kunoko iwo akukhazikika. Rute pa nthawi yomweyo akuyamba kugwira ntchito m’munda, chifukwatu n’nthawi yotuta barele. Mwamuna wochedwa Boazi akum’lola kukunkha barele m’minda yake. Kodi mukudziwa amene anali amake a Boazi? Anali Rahabi wa mu mzinda wa Yeriko.

Tsiku lina Boazi akuuza Rute kuti: ‘Ndamva za iwe, ndi m’mene wakhalira wokoma mtima kwa Naomi. Ndidziwa m’mene unasiyira atate ndi amako ndi dziko lakwanu ndi m’mene unadzakhalira pakati pa anthu osawadziwa ndi kale lonse. Yehova akukomeretu mtima!

Rute akuyankha kuti: ‘Ndinu wokoma mtima kwambiri kwa ine, mbuyanga. Mwandikondweretsa ndi m’mene mwanenera mokoma za ine.’ Boazi akukonda Rute kwambiri, ndipo sipakupita nthawi yaitali asanakwatirane. Ha, ndi zosangalatsa chotani m’mene zimene’zi ziriri kwa Naomi! Koma Naomi ali wachimwemwe kwambiri’di pamene Rute ndi Boazi abala mwana wao woyamba wamwamuna, wochedwa Obedi. Pambuyo pake Obedi akukhala atate wa Davide, za amene tidzaphunzira zochuluka pambuyo pake.

Bukhu la Baibulo la Rute.