Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 51

Rute Ndi Naomi

Rute Ndi Naomi

MU BAIBO muli buku lochedwa Rute. Mu buku limeneli mumapezeka nkhani yokamba za banja lina limene linakhalako pamene oweluza anali kulamulila mu Isiraeli. Rute ni mtsikana amene acokela kudziko la Moabu, ndipo si wa mtundu wa Aisiraeli, mtundu wa Mulungu. Koma pamene Rute aphunzila za Mulungu woona Yehova, ayamba kumukonda kwambili Mulungu. Naomi ni mkazi wacikulile amene anathandiza Rute kuphunzila za Yehova.

Naomi ni mkazi waciisiraeli. Iye, mwamuna wake ndi ana ake amuna aŵili anasamukila kudziko la Moabu, panthawi imene munali njala mu Isiraeli. Ndiyeno tsiku lina, mwamuna wa Naomi anamwalila. Patapita nthawi, ana amuna a Naomi anakwatila atsikana aŵili Acimoabu, Rute ndi Olipa. Koma patapita pafupi-fupi zaka 10, ana aŵili a Naomi nao anafa. Naomi ndi atsikana aŵiliwo anali ndi cisoni kwambili. Kodi Naomi adzacita ciani tsopano?

Tsiku lina Naomi apanga ulendo wobwelela kudziko la kwao. Rute ndi Olipa afuna kukakhala naye, conco apita naye pamodzi. Koma pambuyo poyenda kamtunda, Naomi auza atsikana kuti: ‘Bwelelani kwanu mukakhale ndi amai anu.’

Naomi apsompsona atsikana ndi kuwalaila. Pamenepo atsikana ayamba kulila cifukwa amukonda kwambili Naomi. Iwo akamba kuti: ‘Iyai! Tidzapita nanu kwa anthu anu.’ Koma Naomi awayankha kuti: ‘Bwelelani kwanu, ana anga. Cingakhale bwino mubwelele kwanu.’ Conco Olipa abwelela kwao. Koma Rute safuna kubwelela.

Ndiyeno Naomi auza Rute kuti: ‘Olipa wabwelela kwao. Iwenso ubwelele kwanu.’ Koma Rute ayankha kuti: ‘Musanicondelele kuti nikusiyeni! Nilekeni nipite nanu. Kumene mudzapita, nidzapita, ndipo kumene mudzakhala nidzakhala. Anthu anu adzakhala anthu anga, ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga. Kumene mudzafela, nidzafela kumeneko ndipo nidzaikidwa kumeneko.’ Pamene Rute akamba zimenezi, Naomi aleka kumuuza kuti abwelele kwao.

Potsilizila pake akazi aŵili awa afika ku Isiraeli. Ndipo akhala kumeneko. Posapita nthawi, Rute ayamba kuseŵenza m’minda, popeza ni nthawi yokolola balele. Mwamuna wa dzina lakuti Boazi amulola kuti azikunkha m’minda yake. Kodi udziŵa kuti amai a Boazi anali ndani? Anali Rahabi uja wa ku Yeriko.

Tsiku lina Boazi auza Rute kuti: ‘Ndamva zonse za iwe, ndi zonse zimene unacitila Naomi. Ndamvanso kuti unasiya atate ako, amai ako ndi dziko la abale ako ndi kubwela kudzakhala ndi anthu amene sunali kuwadziŵa. Yehova akudalitse!’

Rute ayankha kuti: ‘Mwanikomela mtima kwambili, mbuyanga. Nakodwa cifukwa ca mau anu wabwino kwa ine.’ Boazi amukonda kwambili Rute, ndipo posapita nthawi io anakwatilana. Zimenezi zikondweletsa Naomi. Akondwela kwambili pamene Rute ndi Boazi abeleka mwana mwamuna woyamba, wa dzina lakuti Obedi. Ndiyeno pambuyo pake Obedi akhala ambuye ake a Davide amene tidzaphunzila zambili za iye mu nkhani za kutsogolo.

Buku la m’Baibo la Rute.