Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 52

Gidiyoni Ndi Asilikali Ake 300

Gidiyoni Ndi Asilikali Ake 300

KODI waona zimene zicitika apa? Onse amuna ali apa ni amuna a nkhondo aciisiraeli. Amuna amene aŵelama akumwa madzi. Mwamuna amene waimilila pafupi nao ni woweluza Gidiyoni. Iye ayang’ana mmene asilikali ake amwela madzi.

Ukayang’anitsitsa udzaona kuti akumwa madzi mosiyana-siyana. Ena acita kuŵelamila pamadzi. Koma wina uyu atapa madzi ndi dzanja, ndipo pakumwa ayang’ana uku ndi uku. Zimenezi n’zofunika cifukwa cakuti Yehova anauza Gidiyoni kusankha cabe amuna amene pakumwa madzi ayang’ana uku ndi uku. Ndipo ena amene sanacite zimenezi, Mulungu anakamba kuti abwelele kunyumba. Tiye tione cifukwa cake.

Aisiraeli alinso pamavuto aakulu cifukwa cakuti sanamvele Yehova. Amidiyani ndi amene awalamulila ndipo awavutitsa kwambili. Conco Aisiraeli alilila kwa Yehova kuti awathandize, ndipo Yehova amvela kulila kwao.

Yehova auza Gidiyoni kuti atenge asilikali, conco Gidiyoni atenga asilikali okwana 32,000. Koma Amidiyani ali ndi asilikali 135,000 ofuna kumenyana ndi Aisiraeli. Ndiyeno Yehova auzanso Gidiyoni kuti: ‘Anthu amene uli nao aculuka kwambili.’ N’cifukwa ciani Yehova anakamba zimenezi?

N’cifukwa cakuti Aisiraeli akapambana nkhondo, angaganize kuti apambana mwa mphamvu zao. Angaganizenso kuti sanafunikile thandizo la Yehova kuti apambane. Conco Yehova auza Gidiyoni kuti: ‘Uza amuna onse amene ali ndi mantha kuti abwelele.’ Pamene Gidiyoni awauza zimenezi, amuna okwana 22,000 abwelela kunyumba. Conco patsala amuna 10,000 cabe amene adzamuthandiza kumenya nkhondo molimbana ndi asilikali 135,000 a ku Midiyani.

Koma mvela zimene Yehova auza Gidiyoni. Iye akuti: ‘Anthu amene uli nao aculuka kwambili.’ Conco Yehova alamula Gidiyoni kuuza amuna a nkhondo kuti ayende ku mtsinje kukamwa madzi, ndi kuti abweze amuna onse amene pakumwa acita kuŵelamila pamadzi. Yehova amulonjeza kuti: ‘Nidzakupulumutsani ndi amuna 300 amene pakumwa madzi anali kuyang’ana uku ndi uku.’

Nthawi ya nkhondo yafika. Ndipo Gidiyoni aika amuna a nkhondo 300 m’magulu atatu. Apatsa munthu aliyense nyanga, ndi mtsuko umene uli ndi nyale mkati mwake. Pakati pa usiku, onse azungulila msasa wa adani. Ndiyeno panthawi imodzi, onse aliza malipenga ndi kuphwanya mitsuko yao, ndipo afuula kuti: ‘Nkhondo ya Yehova ndi Gidiyoni!’ Pamene adani ao auka, asokonezeka ndipo acita mantha. Ndiyeno onse ayamba kuthaŵa, ndipo Aisiraeli awina nkhondo.

Oweruza macaputa 6-8.