Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 53

Lonjezo La Yefita

Lonjezo La Yefita

KODI unalonjezapo cinthu cimene pambuyo pake cinakuvuta kukwanilitsa? Uyu munthu ali apa anacita zimenezo, ndipo ndiye cifukwa cake alila. Mwamuna ameneyu ni woweluza wolimba mtima wa Aisiraeli, dzina lake ni Yefita.

Yefita akhalako panthawi imene Aisiraeli aleka kulambila Yehova. Iwo acitanso vinthu voipa. Conco Yehova alola Aamoni kuti avutitse Aisiraeli. Zimenezi zicititsa Aisiraeli kulilila kwa Yehova kuti: ‘Takucimwilani. Conde, Tipulumutseni!’

Anthu ali ndi cisoni cifukwa ca zinthu zoipa zimene acita. Iwo aonetsa cisoni cao mwa kuyambanso kulambila Yehova. Ndipo Yehova awathandizanso.

Anthu asankha Yefita kuti awatsogolele pamene adzamenyana ndi Aamoni oipa aja. Yefita afunitsitsa kwambili kuti Yehova amuthandize pocita nkhondo. Conco iye alonjeza Yehova kuti: ‘Ngati n’dzapambana Aamoni pankhondo, n’dzapeleka kwa inu munthu woyamba amene adzatuluka m’nyumba yanga kudzanilandila pocokela kunkhondo.’

Yehova wamvela lonjeza la Yefita, ndipo amuthandiza kupambana nkhondo. Kodi umudziŵa munthu woyamba amene atuluka m’nyumba ya Yefita kuti amulandile pamene iye abwelela kucoka kunkhondo? Ni mwana wake mkazi, ndipo iye ndiye mwana wake mmodzi yekha. Pamene Yefita aona mwana wake, alila kuti: ‘Mama ine mwana wanga! Wanibweletsela cisoni. Nalonjeza Yehova ndipo siningasinthe lonjezo langa.’

Pamene mwana wa Yefita akumva za lonjezo limeneli, naye poyamba amvela cisoni. Cifukwa zimenezi zitanthauza kusiya atate ake ndi anzake, ndi kupita kukatumikila Yehova moyo wake wonse, ku cihema ca Yehova ku Silo. Koma auza atate ake kuti: ‘Ngati mwalonjeza Yehova, citani mogwilizana ndi zimene mwalonjeza.’

Conco mwana wa Yefita apita ku Silo, ndipo atumikila Yehova kwa moyo wake wonse pa cihema ca Yehova. Akazi a mu Isiraeli amapita kukamuona masiku anai caka ciliconse, ndipo asangalala naye capamodzi. Anthu amukonda mwana wa Yefita cifukwa ni mtumiki wabwino wa Yehova.

Oweruza 10:6-18; 11:1-40.