Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 57

Mulungu Asankha Davide

Mulungu Asankha Davide

KODI mukuona zimene zachitika? Mnyamata’yo wapulumutsa kamwana ka nkhosa aka ku chimbalangondo. Chimbalangondo’cho chinadza n’chigwira kamwana’ko ndipo chinafuna kukadya. Koma mnyamata’yo anazithamangira nalanditsa kamwana’ko kukamwa kwa chimbalangondo. Pouka chimbalangondo’cho mnyamata’yo anachinyamula nachimenyetsa pansi nachifa! Pa nthawi ina iye anapulumutsa nkhosa kwa mkango. Kodi si mnyamata wolimba mtima? Kodi mukum’dziwa?

Ndiye mnyamata’yo Davide. Iye amakhala m’tauni la Betelehemu. Gogo wake anali Obedi, mwana wa Rute ndi Boazi. Kodi mukuwakumbukira? Ndipo atate wa Davide ndiye Jese. Davide akusamalira nkhosa za atate wake. Davide anabadwa zaka 10 Sauli asanasankhidwe kukhala mfumu.

Nthawi ikudza pamene Yehova akuti kwa Samueli: ‘Tenga mafuta apadera nupite ku nyumba ya Jese m’Betelehemu. Ndasankha mmodzi wa ana ake kukhala mfumu.’ Samueli poona mwana wamkulu wa Jese Eliyabu, akuti: ‘Ndithudi uyu ndiye amene Yehova wam’sankha.’ Koma Yehova akumuuza kuti: ‘Usayang’ane m’mene iyi aliri wamtali ndi wokongola. Sindinam’sankhe kukhala mfumu.’

Chotero Jese akuitana mwana wake Abinadabu nadza naye kwa Samueli. Koma Samueli akuti: ‘Ai, Yehova sanasankhe uyu’nso.’ Kenako, Jese akudza ndi mwana wake Sama. ‘Ai, Yehova sanasankhe uyu’nso,’ akutero Samueli. Jese akudza ndi ana ake asanu ndi awiri kwa Samueli, koma Yehova sakusankha ali yense wa iwo. ‘Kodi awa ndiwo anyamata onse?’ akufunsa motero Samueli.

Jese akuti, ‘pali wina’nso wamng’ono wa onse. Koma iye ali kubusa akuweta nkhosa.’ Pamene Davide akulowetsedwa, Samueli akuona kuti iye ndi mnyamata wokongola. Yehova akuti, ‘Ndi amene’yu. M’tsanulire mafuta.’ Ndipo izi ndizo zimene Samueli akuchita. Nthawi idzafika pamene Davide adzakhala mfumu ya Israyeli.