Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 57

Mulungu Asankha Davide

Mulungu Asankha Davide

KODI waona zimene zacitika? Mnyamata wapulumutsa kamwana ka nkhosa ku cimbalangondo. Pamene cimbalangondo cinabwela cinanyamula kamwana ka nkhosa kuti cikadye. Koma mnyamatayu anacithamangitsa, ndi kupulumutsa kamwana ka nkhosa kuti cisakadye. Ndipo pamene cimbalangondo cinanyamuka, mnyamatayu anacigwila ndi kucimenya ndipo cinafa! Panthawi inanso, mnyamatayu anapulumutsa nkhosa kuti mkango usaidye. Kunena zoona, mnyamatayu ni wolimba mtima! Kodi umudziŵa mnyamata uyu?

Iye ni Davide wacinyamata. Akhala mumzinda wa Betelehemu. Ambuye ake anali Obedi, amene anali mwana wa Rute ndi Boazi. Kodi uwakumbukila amenewa? Ndipo atate a Davide ni a Jese. Davide amalisha mbelele za atate ake. Pamene Yehova anasankha Sauli kukhala mfumu, panapita zaka 10 ndiye pamene Davide anabadwa.

Ndipo nthawi ina Yehova anati kwa Samueli: ‘Tenga mafuta apadela upite kunyumba ya Jese ku Betelehemu. Ndasankha mmodzi wa ana ake kuti akhale mfumu.’ Pamene Samueli aona Eliyabu, mwana mkulu pa onse, iye akuti mu mtima mwake: ‘Ndithudi uyu ni amene Yehova wasankha.’ Koma Yehova amuuza kuti: ‘Usaone maonekedwe ake ndi kutalimpha kwake. Ine sin’namusankhe kuti akhale mfumu.’

Conco Jese aitana mwana wake Abinadabu ndi kubwela naye kwa Samueli. Koma Samueli akuti: ‘Iyai, Yehova sanasankhe uyu.’ Ndiyeno Jese abweletsa mwana wake Shama. Koma Samueli akuti: ‘Iyai, Yehova sanasankhe uyu.’ Jese abweletsa ana ake 7 kwa Samueli, koma Yehova sasankha aliyense pa amenewa. Ndiyeno Samueli afunsa kuti ‘Kodi anyamata anu onse ndi amenewa kwatha?’

Jese akuti: ‘Wamng’ono kwambili sanabwele, pakuti alisha nkhosa.’ Pamene Davide anabwela, Samueli aona kuti iye ni mnyamata wamaonekedwe abwino. Ndiyeno Yehova akuti: ‘Uyu ndiye amene ndasankha, muthile mafuta pamutu.’ Ndipo Samueli acita zimenezi. Nthawi idzafika pamene Davide adzakhala mfumu ya Isiraeli.

1 Samueli 17:34, 35; 16:1-13.