Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 59

Cifukwa Cake Davide Afunikila Kuthaŵa

Cifukwa Cake Davide Afunikila Kuthaŵa

PAMBUYO pakuti Davide wapha Goliyati, mkulu wa gulu la nkhondo la Aisiraeli, Abineri, apeleka Davide kwa Sauli. Sauli akondwela kwambili ndi zimene Davide wacita. Amuika kukhala mkulu wa asilikali ndipo amutenga kuti azikhala naye mu nyumba yacifumu.

Nthawi ina, pamene asilikali abwelako kumene anali kumenyana ndi Afilisti, akazi aimba kuti: ‘Sauli wakantha adani ake masauzande, koma Davide wakantha masauzande makumi-makumi.’ Zimenezi zipangitsa Sauli kucita nsanje cifukwa Davide apatsidwa ulemu waukulu kupambana iye. Koma Yonatani, mwana wa Sauli sanacite nsanje. Iye akonda Davide kwambili, ndipo Davide nayenso amukonda Yonatani. Conco aŵiliwa apangana kuti nthawi zonse adzakhala mabwenzi.

Davide adziŵa kwambili kuimba zeze, ndipo Sauli akonda nyimbo zimene Davide aimba. Koma tsiku lina Sauli anacita cinthu coipa kwambili cifukwa ca nsanje yake. Pamene Davide anali kuimba zeze, Sauli atenga mkondo ndi kuuponya, ndipo anati: ‘Ndilasa Davide ndi kumukhomelela kucipupa.’ Koma Davide alewa, ndipo mkondo uja sunamulase. Panthawi inanso Sauli analephela kulasa Davide ndi mkondo. Conco Davide adziŵa tsopano kuti afunika kukhala wosamala kwambili.

Kodi ukumbukila zimene Sauli analonjeza? Anakamba kuti munthu amene adzapha Goliyati adzamupatsa mwana wake mkazi kuti akhale mkazi wake. Ndiyeno Sauli auza Davide kutenga mwana wake Mikala, koma kuti coyamba afunika kupha adani ao Afilisti okwana 100. Ganiza cabe zimenezo! M’ceni-ceni, Sauli aganiza kuti Afilisti adzapha Davide. Koma io sanamuphe, conco Sauli apeleka mwana wake kuti akhale mkazi wa Davide.

Tsiku lina Sauli auza Yonatani ndi atumiki ake onse kuti afuna kupha Davide. Koma Yonatani auza atate ake kuti: ‘Musamuvulaze Davide, cifukwa iye sanakucimwileni. Koma anakucitilani zinthu zabwino kwambili. Iye anaika moyo wake pangozi pamene anapha Goliyati. Inu munaona zimene zinacitika, ndipo munakondwela.’

Sauli amvela zimene mwana wake akamba, ndipo alonjeza kuti sadzamuvulaza. Davide abwelelanso mu nyumba ya Sauli ndi kupitiliza kutumikila Sauli monga kale. Komabe tsiku lina, pamene Davide ali kuimba zeze, Sauli aponyanso mkondo kuti alase Davide. Koma Davide aulewa, ndipo mkondowo ulasa pacipupa. Imeneyi ni nthawi yacitatu Sauli kucita zimenezi. Conco Davide adziŵa tsopano kuti afunikila kuthaŵa!

Usiku umenewu, Davide apita kunyumba kwake. Koma Sauli atuma anthu kuti apite kumeneko akaphe Davide. Mikala, mkazi wa Davide, adziŵa zimene atate ake afuna kucita. Conco auza mwamuna wake kuti: ‘Ngati simudzapulumutsa moyo wanu usiku uno, mawa mukhala mutaphedwa.’ Usiku umenewo, Mikala athandiza Davide kuthaŵa kucokela pa windo. Kwa zaka pafupi-fupi 7, Davide abisala m’malo osiyana-siyana kuti Sauli asamupeze.

1 Samueli 18:1-30; 19:1-18.