Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 60

Abigayeli Ndi Davide

Abigayeli Ndi Davide

KODI wamudziŵa mkazi wokongola uyu amene akumana ndi Davide? Dzina lake ni Abigayeli. Iye ni wanzelu, ndipo athandiza Davide kuti asacite cinthu coipa. Tikalibe kuphunzila zimenezi, tiye tione zimene zakhala zikucitika kwa Davide.

Pamene Davide athaŵa Sauli, ayenda kukabisala mu phanga kapena kuti mphako. Abale ake ndi banja lonse la atate ake amutsatila. Anthu onse amene abwela kwa iye ni okwana 400, ndipo Davide akhala mtsogoleli wao. Ndiyeno Davide apita kwa mfumu ya Moabu ndipo akuti: ‘Conde, lolani kuti atate ndi amai anga akhale nanu kufikila ndikadziŵa zimene zidzandicitikila.’ Ndiyeno Davide ndi anthu ake ayamba kubisala mu mapili.

Pambuyo pa zimenezi, Davide akumana ndi Abigayeli. Mwamuna wake Nabala ndi wolemela kwambili. Alinso ndi malo ake-ake. Alinso ndi nkhosa 3,000 ndi mbuzi 1,000. Nabala ni wouma mtima. Koma mkazi wake Abigayeli ni wabwino kwambili. Ndiponso adziŵa kucita zinthu zoyenela. Nthawi ina anapulumutsa banja lake lonse. Tiye tione mmene zinacitikila.

Davide ndi anthu ake anakomela mtima Nabala. Anamuthandiza kupulumutsa nkhosa zake. Conco tsiku lina, Davide anatumiza anyamata ake kuti akapemphe thandizo kwa Nabala. Anyamata a Davide afika kwa Nabala pamene iye ndi anchito ake ameta ubweya wa nkhosa. Ni patsiku la phwando, ndipo Nabala ali ndi zakudya zabwino zambili. Conco anyamata a Davide akuti: Tinakukomelani mtima, ndipo sitinabe nkhosa zanu koma tinakuthandizani kuziyan’ganila. Conde tipatsenkoni cakudya tsopano.’

Nabala akuti: ‘Sindingapeleke cakudya canga kwa anthu ngati inu.’ Iye alankhula mouma mtima, ndipo akamba vinthu voipa kwa Davide. Pamene anyamata a Davide abwelela ndi kumuuza zimene Nabala wakamba, Davide akalipa kwambili. Auza anyamata ake kuti: ‘Valani malupanga m’ciuno.’ Pamene atsiliza kucita zimenezi, ayamba ulendo wopita kukapha Nabala ndi anyamata ake.

Koma mmodzi wa anchito a Nabala amene anamva mau oipa a Nabala, apita kukafotokozela Abigayeli zimene zinacitika. Nthawi imeneyo, Abigayeli akonza zakudya. Ndiyeno anyamula zakudyazo pa abulu, ndi kuyamba ulendo wake. Pamene akumana ndi Davide, aseluka pa bulu, ndipo amuwelamila ndi kukamba kuti: ‘Conde mbuyanga, musamvetsele zonena za Nabala mwamuna wanga. Iye alibe nzelu ndipo amacita zinthu zopanda pake. Landilani mphatso iyi, ndipo tikhululukileni cifukwa ca zimene zinacitika.’

Davide ayankha kuti: ‘Ndiwe mkazi wanzelu, ndipo wandithandiza kuti ndisaphe Nabala pofuna kumubwezela kuuma mtima kwake. Pita mwamtendele ku nyumba yako.’ Patapita nthawi, Nabala anamwalila, ndipo Abigayeli anakhala mmodzi wa akazi a Davide.

1 Samueli 22:1-4; 25:1-43.