Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 61

Davide Akulongedwa Ufumu

Davide Akulongedwa Ufumu

SAULI akuyesa’nso kugwira Davide. Akutenga ankhondo ake amphamvu 3,000 namka kukasa-saka Davide. Iye atamva za izi, iye akutumiza azondi kukaona kumene Sauli ndi ankhondo ake agona usiku’wo. Ndiyeno iye akufunsa awiri a amuna ake’wo kuti: ‘Ndani adzafuna kumka nane ku msasa wa Sauli?’

‘Ine,’ Akutero Abisai. Abisai ndi mwana wa mlongo wa Davide Zeruya. Sauli ndi anthu ake ali mtulo, Davide ndi Abisai akulowa mu msasa’wo mwakachetechete. Akutenga mkondo wa Sauli ndi mtsuko wa madzi, umene uli kumutu kwa Sauli. Palibe woona kapena kumva chifukwa iwo onse ali mtulo tatikulu.

Onani Davide ndi Abisai tsopano. Achokapo, afika bwino lomwe pa phiri. Davide akuitana mkulu wankhondo wa Israyeli mopfuula: ‘Abineri, n’chifukwa ninji sukutetezera mbuyako, mfumu? Tayang’ana! Ziri kuti mkondo ndi mtsuko wa madzi za mfumu?’

Sauli akudzambatuka. Akuzindikira mau a Davide, nafunsa kuti: ‘Kodi ndiwe Davide?’ Kodi mukuona Sauli ndi Abineri apo?

‘Inde, mbuyanga mfumu,’ Davide akuyankha Sauli. Nafunsa kuti: ‘Kodi n’cifukwa ninji mukuyesa kundigwira? Kodi ndachita choipa chotani? Nawu mkondo wanu, O mfumu. Tumani mmodzi wa amuna anu adzautenge.’

Sauli akubvomereza kuti, ‘Ndalakwa. Ndachita mopusa.’ Zitatero Davide akuchoka, Sauli nabwerera kwao. Koma Davide akuti mu mtima mwake: ‘Tsiku lina Sauli’yu adzandipha. Ndiyenera kuthawira ku dziko la Afilisti.’ Ndipo anatero’di. Iye akuputsitsa Afilisti n’kuwachititsa kukhulupirira kuti ali ku mbali yao tsopano.

Nthawi ina pambuyo pake Afilisti akumka kukamenyana ndi Israyeli. M’nkhondo, Sauli ndi Jonatani yemwe akuphedwa. Izi zikumvetsa chisoni kwambiri Davide, ndipo akulemba nyimbo yokoma, m’mene iye akuyimba kuti: ‘Ndimva chisoni chifukwa cha iwe, mbale wanga Jonatani. Unalitu wokondedwa kwa ine!’

Pambuyo pake Davide akubwerera ku Israyeli ku mzinda wa Hebroni. Pali nkhondo pakati pa anthu osankha mwana wa Sauli Isiboseti kukhala mfumu ndi anthu ena ofuna Davide kukhala mfumu. Koma potsiriza amuna a Davide akupambana. Davide ali ndi zaka 30 pamene akulongedwa ufumu. Kwa zaka zisanu ndi ziwiri ndi theka iye akulamulira Hebroni. Ena a obadwira kumene’ko akuchedwa Amnoni, Abisalomu ndi Adoniya.

Nthawi ikufika pamene Davide ndi ankhondo ake akumka kukalanda mzinda wokongola wochedwa Yerusalemu. Yoabu, mwana wina wa mlongo wa Davide Zeruya, akutsogolera nkhondo’yo. Chotero Davide akufupa Yoabu mwa kum’panga kukhala mkulu wa gulu lake la nkhondo. Tsopano Davide akuyamba kulamulira mu mzinda wa Yerusalemu.