Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 62

Mavuto M’nyumba Ya Davide

Mavuto M’nyumba Ya Davide

PAMENE Davide ayamba kulamulila mu Yerusalemu, Yehova athandiza asilikali ake kugonjetsa adani ao nthawi zambili. Yehova analonjeza kupatsa Aisiraeli dziko la Kanani. Potsilizila pake, Yehova awathandiza kutenga dziko limene anawalonjeza.

Davide ni wolamulila wabwino, ndipo amakonda Yehova. Conco cinthu coyamba cimene acita pamene alanda Yerusalemu ndico kubweletsa likasa la cipangano la Yehova mu mzinda umenewu. Ndipo afuna kuti amange kacisi moika likasa limeneli.

Pamene Davide akula, alakwitsa zinthu kwambili. Iye adziŵa kuti n’kulakwa kutenga cinthu cimene sicili cake. Koma usiku wina, pamene ali pamtenje wa nyumba yake yacifumu, ayang’ana pansi ndi kuona mkazi wokongola kwambili. Dzina lake ni Batiseba, ndipo mwamuna wake ni Uriya mmodzi wa asilikali a Davide.

Davide amufuna kwambili Batiseba cakuti atuma anthu kuti amubweletse kunyumba yake yacifumu. Koma mwamuna wake palibe ali ku nkhondo. Ndiyeno, Davide agona naye ndipo panthawi ina mkaziyu azindikila kuti ali ndi mimba. Davide akuda nkhawa kwambili, conco atumiza mau kwa mkulu wa asilikali Yoabu. Amuuza kuti aike Uriya kutsogolo pomenya nkhondo kuti aphedwe. Pamene Uriya wafa, Davide akwatila Batiseba.

Yehova akwiyila Davide kwambili. Conco, Yehova atumiza mtumiki wake Natani kuti akauze Davide za macimo ake. Wamuona Natani pacithunzi-thunzi apa pamene akamba kwa Davide? Davide acita cisoni kwambili cifukwa ca zimene wacita. Cifukwa ca kuvomela kulakwa kwake, Yehova sanamuphe. M’malo mwake, amuuza kuti: ‘Cifukwa cakuti wacita zinthu zoipa izi, udzakhala ndi mavuto ambili mu nyumba yako.’ Ndipo Davide akhaladi ndi mavuto ambili!

Coyamba, mwana wa Batiseba amwalila. Ndiyeno mwana woyamba wa Davide Aminoni atenga mlongosi wake Tamara ndi kugona naye mwacikakamizo. Pamene Abisalomu mwana wa Davide amvela zimenezi, akwiya kwambili cakuti akupha Aminoni. Patapita nthawi, anthu ambili amukonda Abisalomu. Poona zimenezi iye adziika kukhala mfumu yao. Potsilizila pake, Davide agonjetsa Abisalomu, ndipo Abisalomu aphedwa. Ndithudi Davide akumana ndi mavuto ambili.

Mkati mwa kucitika kwa zonse izi, Batiseba abala mwana mwamuna, dzina lake Solomo. Pamene Davide akalamba ndipo adwala, mwana wake Adoniya afuna kudziika pa ufumu. Panthawi imeneyo Davide auza wansembe Zadoki kuthila mafuta pa mutu pa Solomo, kuonetsa kuti ndi amene adzakhala mfumu. Pambuyo pake, Davide amwalila ali ndi zaka 70. Analamulila kwa zaka 40. Koma Solomo tsopano ndiye akhala mfumu ya Isiraeli.

2 Samueli 11:1-27; 12:1-18; 1 Mafumu 1:1-48.