Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 64

Solomo Amanga Kacisi

Solomo Amanga Kacisi

DAVIDE akalibe kumwalila, anapatsa Solomo mapulani ocokela kwa Mulungu a mmene angamangile kacisi wa Yehova. Solomo ayamba kumanga kacisi mu caka cacinai ca ulamulilo wake, ndipo atenga zaka 7 ndi hafu kuti atsilize kumanga. Anthu okwana masauzande ambili aseŵenza panchito yomanga kacisi, ndipo pomanga kacisi ameneyu aseŵenzetsa ndalama zambili. Izi zili conco cifukwa cakuti agwilitsila nchito golide ndi siliva wambili pomanga.

Mu kacisi muli zipinda ziŵili zazikulu, monga mmene cihema cinalili. Zipinda za kacisi zimenezi n’zazikulu kuwilikiza kaŵili poyelekeza ndi zipinda za cihema. Solomo aika likasa la cipangano mu cipinda ca mkati ca kacisi, ndipo zinthu zina zimene anali kusungila mu cihema aziika mu cipinda cina.

Pamene atsiliza kumanga kacisi, pakhala cikondwelelo cacikulu. Solomo agwada kutsogolo kwa kacisi ndi kupemphela, monga mmene uonela pacithunzi-thunzi apa. Solomo akuti kwa Yehova: ‘Kumwamba, ngakhale kumwamba-mwamba, simungakwaneko. Nanga kuli bwanji nyumba imene ndamangayi? Komabe, Mulungu wanga, conde mvelani pemphelo la anthu anu limene apemphelela nyumba ino.’

Pamene Solomo atsiliza kupemphela, moto ubwela kucokela kumwamba. Moto umenewo unyeketsa nsembe za nyama zimene zapelekedwa. Ndipo kuwala kwakukulu kocokela kwa Yehova kudzaza kacisi. Zimenezi zionetsa kuti Yehova amvetsela, ndi kuti akondwela ndi kacisi ndi pemphelo la Solomo. Tsopano kacisi akhala malo kumene anthu ayendako kukalambila m’malo moyenda kucihema.

Kwa nthawi yaitali Solomo alamulila mwanzelu, ndipo anthu akondwela. Koma m’kupita kwa nthawi, Solomo akwatila akazi ambili amene samalambila Yehova, ocokela kumaiko ena. Kodi wamuona mkazi wake wina amene apembedza fano pacithunzi-thunzi apa. Potsilizila pake, akazi ake amucititsa kuti naye ayambe kulambila milungu ina. Kodi udziŵa zimene zicitika pamene Solomo acita zimenezi? Iye aleka kulamulila anthu mokoma mtima, ndipo akhala wankhanza, cakuti anthu salinso okondwela.

Zimenezi zicititsa Yehova kukwiyila Solomo, ndipo amuuza kuti: ‘N’dzakulanda ufumu ndi kuupeleka kwa munthu wina. Sinidzacita zimenezi iwe uli moyo, koma pamene mwana wako adzayamba kulamulila. Ndipo mu ufumu wa mwana wako, sinidzamulanda anthu onse.’ Tiye tione mmene zimenezi zinacitikila.

1 Mbiri 28:9-21; 29:1-9; 1 Mafumu 5:1-18; 2 Mbiri 6:12-42; 7:1-5; 1 Mafumu 11:9-13.