Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 66

Yezebeli—mfumukazi Yoipa

Yezebeli—mfumukazi Yoipa

PAMENE Mfumu Yeroboamu amwalila, mfumu iliyonse imene ilamulila mafuko 10 a Isiraeli akumpoto ni yoipa. Mfumu Ahabu ndiye woipa kwambili pa mafumu onse. Kodi udziŵa cifukwa cake? Cifukwa cacikulu ni mkazi wake Yezebeli, amene ni mfumukazi yoipa.

Yezebeli si mkazi waciisraeli. Ni mwana wa mfumu ya ku Sidoni. Iye alambila mulungu wonama Baala, ndipo acititsa Ahabu ndi Aisiraeli ambili kuti naonso ayambe kulambila Baala. Yezebeli amazonda Yehova, ndipo akupha aneneli a Yehova ambili. Ena abisama mu mphako kuti asaphedwe. Ngati Yezebeli afuna cinacake, akhoza ngakhale kupha munthu kuti apeze cimene afuna.

Tsiku lina Mfumu Ahabu anali ndi cisoni kwambili. Conco Yezebeli amufunsa kuti: ‘N’cifukwa ciani lelo muoneka wacisoni?’

Ahabu ayankha kuti: ‘N’cifukwa ca zimene Naboti wandiuza. Ndinafuna kugula munda wake wa mpesa, koma ananiuza kuti sanganigulitse.’

Yezebeli akuti: ‘Osadandaula, ine n’dzakutengelani munda umenewo kwa Naboti.’

Conco Yezebeli alembela makalata akulu ena amene akhala mu mzinda umodzi ndi Naboti. Iye awauza kuti: ‘Pezani amuna opanda pake kuti akanene kuti Naboti watembelela Mulungu ndi Mfumu. Ndiyeno mukamutulutse kunja kwa mzinda ndi kumuponya miyala kuti akafe.’

Pamene Yezebeli adziŵa kuti Naboti wafa, auza Ahabu kuti: ‘Yendani tsopano mukatenge munda wa mpesa.’ Kodi uvomeleza kuti Yezebeli afunika kupatsidwa cilango cifukwa cocita cinthu coipa cimeneci?

Conco m’kupita kwa nthawi, Yehova atumiza Yehu kuti akalange Yezebeli. Pamene Yezebeli amvela kuti Yehu abwela, apenta maso ake ndi kudzikonza-konza kuti aoneke wokongola. Koma pamene Yehu afika ndi kuona kuti Yezebeli ali pa windo, afuula kwa amuna amene ali mu nyumba ya mfumu kuti: ‘M’ponyeni pansi!’ Amunawo acita zimene auzidwa, monga mmene uonela pacinthunzi-thunzi apa. Iwo amuponya pansi ndipo akufa. Amenewa ndiwo mapeto a Yezebeli Mfumukazi yoipa.

1 Mafumu 16:29-33; 18:1-4; 21:1-16; 2 Mafumu 9:30-37.