NKHANI 67
Yehosafati Adalira Yehova
KODI mukudziwa amuna’wa ndi zimene iwo akuchita? Iwo akumka ku nkhondo, ndipo amuna ali patsogolo’wo akuyimba. Koma mungafunse kuti: ‘Nchifukwa ninji oyimba’wo alibe malupanga ndi mikondo zomenyera nkhondo?’ Tiyeni tione.
Yehosafati ndiye mfumu ya ufumu wa mafuko awiri wa Israyeli. Iye akukhala ndi moyo pa nthawi imodzi-modzi ndi Mfumu Ahabu ndi Yezebeli ya ufumu wakumpoto wa mafuko 10. Koma Yehosafati ndi mfumu yabwino, ndipo atate wake Asa anali’nso mfumu yabwino kwambiri. Kwa zaka zambiri anthu a ufumu wakumwela wa mafuko awiri analinkukhala bwino.
Komano kanthu kena kakuchitika kochititsa anthu’wo mantha. Amithenga akusimbira Yehosafati kuti: ‘Gulu la nkhondo lalikulu lochokera ku maiko a Moabu, Amoni, ndi Phiri la Seiri akudza kudzakuukirani.’ Aisrayeli ambiri akusonkhana pa Yerusalemu kudzafuna chithandizo cha Yehova. Akumka ku kachisi, kumene’ko Yehosafati akupemphera kuti: ‘O Yehova Mulungu wathu, sitikudziwa chochita. Tathedwa nzeru ndi gulu la nkhondo lalikulu’li. Tikuyang’ana kwa inu kaamba ka chithandizo.’
Yehova akumvetsera, ndipo akutuma mmodzi wa atumiki ake kuuza anthu’wo kuti: ‘Nkhondo’yi si yanu, koma ya Mulungu. Simudzamenya. Ingopenyani, muone m’mene Yehova adzakupulumutsirani.’
Tsono m’mawa mwake Yehosafati akuwauza kuti: ‘Dalirani Yehova!’ Ndiyeno akuika oyimba patsogolo pa ankhondo’wo, ndipo pamene akuguba akuyimba zitamando kwa Yehova. Kodi mukudziwa chimene chikuchitika poyandikira ku nkhondo’ko? Yehova akuchitititsa ankhondo a adani’wo kumenyana okha-okha. Pofika iwo, wankondo ali yense wa adani’wo wafa!
Kodi sikunali kwanzeru kwa Yehosafati kudalira Yehova? Tidzakhala anzeru tikadalira Yehova.