Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 69

Mtsikana Athandiza Ngwazi

Mtsikana Athandiza Ngwazi

KODI mukudziwa zimene buthu’li likunena? Likuuza mai’yo za mneneri wa Yehova Elisa, ndi zodabwitsa zimene Yehova amam’thandiza kuchita. Mai’yo sakudziwa za Yehova chifukwa si Wachiisrayeli. Tiyeni tsono tione, chifukwa chake mtsikana’yu ali m’nyumba ya mai’yu.

Mai’yo ndi Msuri. Mwamuna wake ndiye Namani, mkulu wa gulu la nkhondo la Asuri. Asuri anagwira buthu Lachiisrayeli’li, nalipereka kwa mkazi wa Namani kukhala mdzakazi wake.

Namani ali n’thenda yoipa yochedwa khate. Nthenda’yi imanyonyotsola minofu ya munthu. Choncho izi ndizo zimene likuuza mkazi wa Namani: ‘Mbuyanga akanangopita kwa mneneri wa Yehova ali m’Israyeli. Akanakachiritsidwa naye khate’li.’ Kenako mai’yo akuuza mwamunake zimene kabuthu’ko kananena.

Namani akufuna kwambiri kuchiritsidwa; chotero akusankha kumka ku Israyeli. Atafika’ko, akumka ku nyumba ya Elisa. Elisa akutuma mtumiki wake kukauza Namani kukasamba m’Yordano kasanu ndi kawiri. Izi zikupsyetsa mtima Namani, nati: ‘Mitsinje ya kwathu iri yabwino kwambiri koposa mtsinje uli wonse mu Israyeli!’ Atatero, Namani akuchoka.

Koma mmodzi wa atumiki ake akumuuza kuti: ‘Mbuyanga, Elisa akadakuuzani kuchita kanthu kobvuta, mukanakachita. Nangano bwanji osangosamba, monga momwe wanenera?’ Namani akumvetsera mtumiki wake napita kukadzibviika mu Mtsinje wa Yordano kasanu ndi kawiri. Pamene akutero, mnofu wake ukulimba ndi kukhala wathanzi!

Namani ali wokondwa kwambiri. Akubwerera kwa Elisa namuuza kuti: ‘Tsopano ndadziwa’di kuti Mulungu wa mu Israyeli ndiye Mulungu yekha woona pa dziko lonse. Chotero, chonde, landirani mphatso’yi kwa ine.’ Koma Elisa akuyankha kuti: ‘Ai, sindidzailandira.’ Elisa akudziwa kuti kukakhala kolakwa kwa iye kulandira mphatso’yo, chifukwatu ndiye Yehova amene wachiritsa Namani. Koma mtumiki wa Elisa Gehazi akudzifunira mphatso’yo.

Chotero nazi zimene Gehazi akuchita. Atachoka Namani, Gehazi akum’thamangira. ‘Elisa wandituma kudzakuuzani kuti akufuna zina za mphatso yanu kaamba ka mabwenzi amene angofika kumene,’ akutero Gehazi. Ndithudi, iri ndi bodza. Koma Namani sakudziwa kuti ndi bodza; chotero akupatsa Gehazi zina za zinthu’zo.

Pobwerera kunyumba Gehazi, Elisa akudziwa zimene wachita. Yehova wamuuza. Chotero akuti: ‘Chifukwa chakuti unachita choipa’chi, khate la Namani lidzakhala pa iwe.’ Ndipo linatero, pompo!

Kodi tingaphunzirenji m’zonse’zi? Choyamba, kuti tiyenera kukhala ngati buthu’li ndi kulankhula za Yehova. Kungachite zabwino kwambiri. Chachiwiri, sitiyenera kukhala onyada ngati Namani poyamba, koma tiyenera kumvera atumiki a Mulungu. Ndipo chachitatu, sitiyenera kunana ngati momwe anachitira Gehazi. Kodi sitingaphunzire zochuluka mwa kuwerenga Baibulo?