Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 70

Yona Ndi Cinsomba

Yona Ndi Cinsomba

ONA mwamuna uyu amene ali m’madzi. Aoneka kuti wavutika kwambili, si conco? Cinsomba ici cifuna kumumeza! Kodi wamudziŵa mwamuna ameneyu? Dzina lake ni Yona. Tiye tione cimene cinacititsa kuti akhale m’mavuto akulu conco.

Yona ni mneneli wa Yehova. Pakalibe kupita nthawi itali kucokela pamene mneneli Elisa anamwalila, Yehova auza Yona kuti: ‘Pita kumzinda waukulu wa Nineve. Anthu akucita zinthu zoipa kwambili kumeneko, ndipo nifuna ukawauze za kuipa kwao.’

Koma Yona safuna kuyendako. M’malo mwake, akwela boti imene iyenda kwina osati ku Nineve. Yehova wakalipa pamene Yona wathawa. Conco Yehova abweletsa cimphepo camphamvu kwambili, cakuti boti ifuna kumbila. Oyendetsa botiwo acita mantha kwambili, ndipo afuulila kwa milungu yao kuti iwathandize.

Potsilizila pake, Yona awauza kuti: ‘Ine ndimalambila Yehova, Mulungu amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi. Ndipo ndathawa kucita zimene Yehova anandiuza.’ Conco oyendetsa botiwo afunsa kuti: ‘Ticite nawe ciani kuti cimphepo cileke?’

Yona akuti: ‘Niponyeni mu nyanja, ndipo nyanjayi idzakhalanso bata.’ Oyendatsawo safuna kucita zimenezi, koma pamene aona kuti cimphepo cionjezeleka, anyamula Yona ndi kumuponyela mu nyanja. Nthawi imeneyo, cimphepo cileka, ndipo nyanja ikhalanso bata.

Pamene Yona ambila m’madzi, cinsomba cikulu cimumeza, koma sanafe. Akhala m’mimba mwa cisomba kwa masiku atatu. Yona acita cisoni kwambili kuti sanamvele Yehova, ndipo sanayende ku Nineve. Kodi udziŵa zimene iye acita?

Yona apemphela kwa Yehova kuti amuthandize. Ndiyeno Yehova acititsa cinsomba kulavulila Yona kumbali kwa nyanja. Pambuyo pake Yona ayenda ku Nineve. Kodi zimenezi sizitiphunzitsa kuti n’kofunika kucita zilizonse zimene Yehova atiuza?

Macaputa onse a buku la Yona.