Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 71

Mulungu Alonjeza Paradaiso

Mulungu Alonjeza Paradaiso

CHINTHUNZI’CHI n’cha paradaiso wonga amene Mulungu angakhale atasonyeza mneneri wake Yesaya. Yesaya anakhala ndi moyo pambuyo pa Yona.

Paradaiso amatanthauza “munda” kapena “paki.” Kodi zikukukumbutsani za kanthu kena kamene takaona m’bukhu’li? Akuoneka mofanana kwambiri ndi munda wokongola umene Yehova Mulungu anapangira Adamu ndi Hava, kodi si choncho? Koma kodi dziko lonse lidzakhala paradaiso?

Yehova anauza mneneri wake Yesaya kulemba za paradaiso akudza’yo kaamba ka anthu a Mulungu. Iye akuti: ‘Mimbulu ndi nkhosa zidzakhalira pamodzi mu mtendere. Ana a ng’ombe ndi ana a mikango zidzadyera pamodzi, ndipo ana ang’ono adzazitsogolera. Ngakhale khanda silidzabvulazidwa ngati lisewera ndi njoka yaululu.’

‘Izi sizidzachitika konse’ ambiri angatero. ‘Nthawi zonse pakhala bvuto pa dziko lapansi, ndipo lidzakhalapo nthawi zonse.’ Koma taziganizireni: Kodi Mulungu anapatsa malo okhala otani kwa Adamu ndi Hava?

Mulungu anaika Adamu ndi Hava m’paradaiso. N’chifukwa chabe chakuti iwo sanamvere Mulungu kuti iwo anataya malo ao okhala okongola’wo, anakalamba ndi kufa. Mulungu akulonjeza kuti adzapatsa anthu amene anam’konda zinthu zeni-zeni’zo zimene Adamu ndi Hava anataya.

M’paradaiso watsopano akudza’yo palibe chiri chonse chidzabvulaza kapena kuononga. Padzakhala mtendere weni-weni. Anthu onse adzakhala athanzi ndi achimwemwe. Koma tidzaphunzirabe m’mene Mulungu adzachititsira zimene’zi.