Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 72

Mulungu Athandiza Mfumu Hezekiya

Mulungu Athandiza Mfumu Hezekiya

KODI udziŵa cifukwa cake mwamuna uyu apemphela kwa Yehova? N’cifukwa ciani waika makalata aya patsogolo pa guwa la Yehova? Mwamuna uyu ni Hezekiya. Iye ni mfumu ya mafuko aŵili akum’mwela aciisiraeli. Ndipo avutika maganizo kwambili. Cifukwa ciani?

Cifukwa cakuti asilikali a Asuri aononga kale mafuko 10 akumpoto. Yehova alola kuti zimenezi zicitike cifukwa anthu amenewa ni oipa kwambili. Ndipo gulu la nkhondo la Asuri tsopano labwela kudzacita nkhondo ndi ufumu wa mafuko aŵili.

Mfumu ya Asuri yangotumiza makalata kwa mfumu Hezekiya. Makalata amenewa ni amene Hezekiya waika pamaso pa Mulungu monga mmene waonela pacithunzi-thunzi apa. M’makalata amenewa alembamo zonyoza Yehova ndi zoopseza Hezekiya. N’cifukwa cake Hezekiya apemphela kuti: ‘O Yehova, tipulumutseni kwa Mfumu ya Asuri. Pamenepo mitundu yonse idzadziŵa kuti inu nokha ndinu Mulungu.’ Kodi Yehova adzamvetsela kwa Hezekiya?

Hezekiya ni mfumu yabwino. Iye sali monga mafumu oipa a ufumu wa mafuko 10 a Isiraeli, kapena monga tate wake, Mfumu Ahazi amene anali woipa. Hezekiya amatsatila malamulo onse a Yehova mosamala. Conco, Pamene Hezekiya atsiliza kupemphela, mneneli Yesaya amutumizila uthenga wocokela kwa Yehova wakuti: ‘Mfumu ya Asuri sidzabwela ku Yerusalemu. Palibe ngakhale msilikali wake amene adzafika pafupi ndi iye. Sadzaponya muvi uliwonse mumzinda.’

Ona cithunzi-thunzi cimene cili papeji iyi. Kodi asilikali akufa onsewa waŵadziŵa? Amenewa ni Asuri. Yehova anatuma mngelo wake, ndipo usiku umodzi cabe mngeloyo anapha asilikali a Asuri okwana 185,000. Pamenepo mfumu ya Asuri ileka kucita nkhondo ndipo ibwelela kwao.

Ufumu wa mafuko aŵili upulumutsidwa, ndipo anthu akhala pamtendele kwa kanthawi. Koma pamene Hezekiya amwalila, mwana wake Manase ndiye akhala mfumu. Manase ndi Amoni mwana wake amene akhala mafumu pambuyo pake, onse aŵili ni mafumu oipa kwambili. Conco dziko lidzalanso ndi upandu ndi ciwawa. Pamene Amoni aphedwa ndi atumiki ake, Mwana wake Yosiya ndiye akhala mfumu ya ufumu wa mafuko aŵili.

2 Mafumu 18:1-36; 19:1-37; 21:1-25.