Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 73

Mfumu Yabwino Yomaliza

Mfumu Yabwino Yomaliza

YOSIYA ali ndi zaka zisanu ndi zitatu zokha pamene iye akukhala mfumu ya mafuko awiri a kumwela a Israyeli. Uwu ndi usinkhu wochepa kwambiri woti munthu n’kukhala mfumu. Chotero poyamba anthu achikulire akum’thandiza kulamula mtundu’wo.

Yosiya atakhala mfumu kwa zaka zisanu ndi ziwiri akuyamba kufuna-funa chithandizo cha Yehova. Iye akutsatira chitsanzo cha mafumu abwino onga ngati Davide, Yehosafati ndi Hezekiya. Ndiyeno, akali kamnyamatabe, Yosiya akuchita chinthu chosonyeza kulimba mtima.

Kwa nthawi yaitali Aisrayeli ochuluka akhala oipa kwambiri. Iwo akulambira milungu yonyenga. Iwo akugwadira mafano. Chotero Yosiya akumka ndi amuna ake nayamba kuchotsa kulambira konyenga m’dziko’lo. Iyi n’ntchito yaikulu chifukwa anthu ochuluka akulambira milungu yonyenga. Mungaone Yosiya uyo ndi anthu ake akuphwanya mafano.

Pambuyo pake, iye akuika amuna atatu kuyang’anira ntchito yokonza kachisi. Ndalama zikusonkhedwa kuchokera kwa anthu n’kuperekedwa kwa amuna’wa kuti alipirire ntchito imene iyenera kuchitidwa. Akadagwira ntchito pa kachisi’yo, mkulu wansembe Hilikiya akupeza kanthu kena kofunika kwambiri m’menemo. Ndiro bukhu leni-leni la chilamulo chimene Yehova ananinkha Moses kuchilemba kale-kale’lo. Linali litatayika kwa zaka zambiri.

Bukhu’lo likuperekedwa kwa Yosiya, ndipo iye akupempha am’werengere. Pamene akumvetsera, iye akuona kuti anthu akhala asakusunga chilamulo cha Yehova. Iye akumva nazo chisoni kwambiri, chotero akung’amba zobvala zake, monga momwe mukuonera pano. Iye akuti: ‘Yehova watikwiyira, chifukwa chakuti atate wathu sanasunge malamulo olembedwa m’bukhu’li.

Yosiya akulamula mkulu wa ansembe Hilikiya kupeza zimene Yehova adzawachitira. Hilikiya akumka kwa mkazi’yo Hulida, amene ali mneneri wachikazi, nam’funsa. Iye akum’patsa uthenga uwu wochokera kwa Yehova woti akapereke kwa Yosiya: ‘Yerusalemu ndi anthu onse adzalangidwa chifukwa chakuti iwo alambira milungu yonyenga ndipo dziko’lo ladzazidwa ndi kuipa. Koma chifukwa chakuti iwe, Yosiya, wachita zabwino, chilango ichi sichidzadza kufikira iwe utafa.’