Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 75

Anyamata Anai Ku Babulo

Anyamata Anai Ku Babulo

MFUMU Nebukadinezara itenga Aisiraeli onse ophunzila bwino kwambili ndi kupita nao ku Babulo. Pambuyo pake, Mfumu isankhapo anyamata okongola ndi anzelu kwambili. Anai mwa amenewa ni anyamata amene uona pacithunzi-thunzi apa. Mmodzi ni Danieli ndipo atatuwo, Ababulo amawacha kuti Sadirake, Mesake ndi Abedinego.

Nebukadinezara afuna kuphunzitsa anyamatawa kuti azitumikila mu nyumba yake yacifumu. Pambuyo powaphunzitsa kwa zaka zitatu, iye adzasankhapo cabe amene adzaonetsa kuti ali ndi nzelu kwambili, kuti azimuthandiza kuthetsa mavuto. Iye afuna kuti anyamata akhale amphamvu ndi athanzi labwino pamene aphunzitsidwa. Conco alamula anchito ake kuti azipatsa anyamata onse zakudya zabwino ndi vinyo, zofanana ndi zimene iye ndi banja lake amadya.

Ona Danieli ali mnyamata pacithunzi-thunzi apa. Kodi udziŵa zimene auza Asipenazi, mkulu wa anchito a Nebukadinezara? Danieli amuuza kuti safuna kudya zakudya zabwino za mfumu. Koma Asipenazi akuda nkhawa. Iye akamba kuti: ‘Mfumu yakusankhilani zimene muyenela kudya ndi kumwa. Ndipo ngati simudzaoneka athanzi monga anyamata ena, idzanipha.’

Conco Danieli apita kwa munthu amene Asipenazi wamuika kuti aziyang’anila Danieli ndi anzake aja atatu. Iye amuuza kuti: ‘Conde, tiyeseni kwa masiku 10. Muzitipatsa zakudya zamasamba ndi madzi akumwa. Ndiyeno pambuyo pake mukatilinganize ndi anyamata ena amene akudya zakudya zabwino za mfumu, kuti mukaone amene adzaoneka bwino.’

Munthu amene awayang’anila avomela kucita zimenezi. Ndipo pamene masiku 10 akwana, Danieli ndi anzake atatu aoneka athanzi labwino kwambili kuposa anyamata ena onse. Conco munthu wowayang’anila awalola kuti apitilize kudya zamasamba m’malo mwa zakudya zimene mfumu iwapatsa.

Pamene zaka zitatu zikwana, anyamata onse apelekedwa kwa Nebukadinezara. Pambuyo pokambitsilana ndi anyamata onse, iye apeza kuti Danieli ndi anzake atatu, ndio anzelu kuposa anyamata onse. Conco awasunga kuti azithandiza mu nyumba ya mfumu. Ndipo nthawi iliyonse imene mfumu ifunsa mafunso kapena kuwapatsa nchito zovuta kwambili, Danieli, Sadirake, Mesake ndi Abedinego, adziŵa bwino kwambili nthawi kuŵilikiza 10, kuposa ansembe onse kapena amuna ake anzelu onse.

Danieli 1:1-21.