Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 79

Danieli m’Dzenje la Mikango

Danieli m’Dzenje la Mikango

O, O! KUKUONEKERA ngati Danieli ali m’bvuto lalikulu. Koma mikango’yo sikum’bvulaza! Kodi mukudziwa chifukwa chake? Kodi ndani waika Danieli muno ndi mikango yonse’yi? Tiyeni tione.

Mfumu ya Babulo tsopano ndi munthu wochedwa Dariyo. Iye amakonda Danieli kwambiri chifukwa chakuti ndi wokoma mtima ndi wanzeru. Dariyo akum’sankha kukhala wolamulira wamkulu mu ufumu wake. Izi zikupangitsa nsanje amuna ena mu ufumu’wo, chotero nazi zimene akuchita.

Akumka kwa Dariyo namuuza kuti: ‘Tabvomerezana, O mfumu, kuti mupange lamulo lakuti kwa masiku 30 pasakhale munthu wopemphera kwa mulungu wina ali yense kusiyapo kwa inu, O mfumu. Ngati wina samvera, ayenera kuponyedwa m’dzenje la mikango.’ Dariyo sakudziwa chifukwa chake amuna’wa akufuna kuti lamulo’li lipangidwe. Koma akuganiza kuti ndi lingaliro labwino, chotero akulemba lamulo’lo. Tsopano lamulo’lo silingasinthidwe.

Danieli atamva lamulo’lo, akumka kwao napemphera, monga mwa masiku onse. Oipa’wo anadziwa kuti Danieli sakaleka kupemhera kwa Yehova. Iwo ali okondwa, chifukwa akuona kuti kakonzedwe kao ka kum’pha kadzatheka.

Mfumu Dariyo atamva chifukwa chake amuna’wa anafuna kupanga lamulo’li, akumva chisoni. Koma sangasinthe lamulo’lo, chotero ayenera kulamula kuti Danieli aponyedwe m’dzenje la mikango.’ Koma mfumu’yo ikuuza Danieli kuti: ‘Ndiganiza kuti Mulungu wako, amene um’tumikira, adzakupulumutsa.’

Dariyo ali wobvutika maganizo kwambiri kwakuti sakuona tulo usiku’wo. M’mawa mwake akuthamangira ku dzenje la mikango’lo. Mungamuone apo. Iye akuitana mopfuula kuti: ‘Danieli, mtumiki wa Mulungu wamoyo! Kodi Mulungu amene unam’tumikira wakupulumutsa ku mikango’yo?’

Danieli akuti, ‘Mulungu anatumiza mngelo wake natseka pakamwa pa mikango kwakuti sinandipweteke.’

Iye ali wokondwa kwambiri. Akulamula kuti atulutsidwemo. Ndiyeno akulamula kuti ofuna kupha Danieli’wo aponyedwemo. Asanafike n’komwe pansi, mikango’yo ikuwawakha ndi kuwapwepweta ndi mafupa omwe.

Dariyo akulembera kalata anthu onse a mu ufumu wake kuti: ‘Ndikulamulira kuti ali yense alemekeze Mulungu wa Danieli. Amachita zozizwitsa. Wapulumutsa Danieli osadyedwa ndi mikango.’