Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 81

Kudalila Thandizo La Mulungu

Kudalila Thandizo La Mulungu

PAFUPI-FUPI anthu 50,000 ayenda ulendo wautali wocokela kuti Babulo kubwelela ku Yerusalemu. Koma pamene afika, apeza kuti Yerusalemu ni bwinja cabe, kapena kuti matongwe. Kulibe munthu amene akhalako. Aisiraeli afunika kuyambanso kumanga zonse.

Cinthu coyamba cimene io amanga ni guwa la nsembe. Awa ni malo opelekelapo nsembe, kapena kuti mphatso za nyama kwa Yehova. Pambuyo pa miyezi yocepa Aisiraeli ayamba kumanga kacisi. Koma adani amene akhala m’mizinda yapafupi safuna kuti Aisiraeli amange kacisi. Conco ayamba kuwaopseza kuti aleke. Potsilizila pake, adani amenewa asonkhezela mfumu yatsopano ya Perisiya kupanga lamulo loletsa nchito yomanga.

Zaka zambili zipita, ndipo tsopano papita zaka 17 kucokela pamene Aisiraeli anacoka ku Babulo. Yehova atuma aneneli ake Hagai ndi Zekariya kuuza anthu kuti ayambenso nchito yomanga. Anthu adalila thandizo la Yehova, ndipo amvela aneneli. Iwo ayambanso kumanga ngakhale kuti lamulo likamba kuti asamange.

Conco nduna yaciperisiya yochedwa Tatenai ibwela, ndipo ifunsa Aisiraeli kumene acotsa mphamvu zakuti amange kacisi. Aisiraeli aiuza kuti pamene anali ku Babulo, Mfumu Koresi inawauza kuti: ‘Tsopano pitani, ku Yerusalemu mukamange kacisi wa Yehova, Mulungu wanu.’

Tatenai atumiza kalata ku Babulo ndi kufunsa ngati Koresi, amene tsopano anamwalila, anakambadi zimenezo. Posapita nthawi mfumu yatsopano ya Perisiya iyankha kalatayo. Ndipo ivomeleza kuti n’zoona Koresi anakamba zimenezo. Ndipo mfumu ilemba kuti: ‘Aleke Aisiraeli amangile Mulungu wao kacisi. Ndipo nilamula iwe kuti uwathandize.’ M’zaka pafupi-fupi 4 atsiliza kumanga kacisi, ndipo Aisiraeli akondwela kwambili.

Zaka zambili zipita, ndipo tsopano papita zaka 48 kucokela pamene kacisi anamangidwa. Anthu ku Yerusalemu ni osauka, ndipo mzinda pamodzi ndi kacisi wa Mulungu sizioneka bwino. Kumene ali ku Babulo, Ezara Mwisiraeli amvela za nchito yokonza kacisi wa Mulungu. Kodi udziŵa zimene acita?

Ezara apita kukaona Mfumu ya Perisiya Aritasasta, ndipo Mfumu yabwino imeneyi ipatsa Ezara mphatso zambili kuti apeleke ku Yerusalemu. Ezara apempha Aisiraeli ali ku Babulo kuti amuthandize kupeleka mphatso zimenezi ku Yerusalemu. Anthu pafupi-fupi 6,000 avomela kupita. Ali ndi siliva wambili, golide wambili ndi zinthu zina zamtengo wapatali zambili zakuti atenge poyenda.

Ezara ali ndi nkhawa, cifukwa mu njila muli anthu oipa. Anthu oipa amenewa angawaphe ndi kutenga siliva ndi golide. Conco, Ezara asonkhanitsa anthu, monga mmene uonela pacithunzi-thunzi apa. Ndiyeno apemphela kwa Yehova kuti awachinjilize paulendo wao wautali wobwelela ku Yerusalemu.

Yehova awachinjiliza. Ndipo pambuyo pa ulendo wa miyezi 4, io afika bwino-bwino ku Yerusalemu. Kodi zimenezi sizionetsa kuti Yehova amachinjiliza anthu amene amadalila thandizo lake?

Ezara macaputa 2 mpaka 8.