Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 82

Mordekai Ndi Estere

Mordekai Ndi Estere

TIYE tibwelele kumbuyo pang’ono pamene Ezara akalibe kuyenda ku Yerusalemu. Mordekai ndi Estere ni Aisiraeli amene ali ndi maudindo akulu kwambili mu ufumu wa Aperisiya. Estere ni mfumukazi, ndipo msuweni wake Mordekai ni waciŵili kwa mfumu. Tiye tione mmene zimenezi zinacitikila.

Makolo a Estere anafa pamene iye anali mng’ono kwambili, conco Mordekai ndiye anamusunga. Ahasiwero, mfumu ya Aperisiya, ali ndi nyumba yake yacifumu ku mzinda wa Susani, ndipo Mordekai ni mmodzi wa anchito ake. Ndiyeno tsiku lina mkazi wa mfumu Vasiti acita cinthu colakwa, conco mfumu isankha mkazi wina watsopano kuti akhale mfumukazi. Kodi ungamudziŵe mkazi amene isankha? Isankha Estere mkazi wacicepele wokongola.

Wamuona mwamuna wonyada amene anthu agwadila? Uyu ni Hamani, ni munthu waudindo waukulu mu Perisiya. Hamani afuna Mordekai, amene akhala apa, kuti nayenso amugwadile. Koma Mordekai sacita zimenezo. Iye aona kuti ni cosayenela kugwadila munthu woipa ameneyu. Zimenezi zipangitsa Hamani kukalipa kwambili. Kodi udziŵa zimene acita?

Hamani auza mfumu mabodza ponena za Aisiraeli. Iye akamba kuti: ‘Aisiraeli ni anthu oipa amene samamvela malamulo anu, conco ayenela kuphedwa.’ Ahasiwero sadziŵa kuti mkazi wake Estere ni Mwisiraeli. Conco amvela zimene Hamani akamba, ndipo aika lamulo lakuti patsiku lina lake Aisiraeli onse akaphedwe.

Pamene Mordekai amvela za lamulo limeneli, akalipa kwambili. Atumiza mau kwa Estere kuti: ‘Ukambe ndi mfumu, ndipo uicondelele kuti itipulumutse.’ Ni kuphwanya lamulo mu Perisiya kupita kukaona mfumu popanda kuitanidwa. Koma Estere apita popanda kuitanidwa. Mfumu imusontha ndi ndodo yake yagolide, zimene zitanthauza kuti sayenela kuphedwa. Estere aitanila mfumu ndi Hamani ku cakudya. Ndipo ali kumeneko mfumu ifunsa Estere cimene afuna kuti imucitile. Estere akuti adzakamba pamene mfumu idzabwelanso pamodzi ndi Hamani ku cakudya cina tsiku lotsatila.

Pamene akudya cakudya patsiku lotsatila, Estere auza mfumu kuti: ‘Ine ndi anthu anga tidzaphedwa.’ Mfumu ikalipa ndipo ifunsa kuti: ‘Ndani afuna kucita zimenezi?’

Estere ayankha kuti: ‘Mdani, munthu woipa ameneyu ni Hamani!’

Tsopano mfumu ikalipa kwambili. Ndipo ilamula kuti Hamani aphedwe. Pambuyo pake mfumu iika Mordekai kukhala waciŵili kwa iye. Ndiyeno Mordekai atsimikiza kuti apanga lamulo latsopano limene lidzalola Aisiraeli kukadzichinjiliza patsiku limene ayenela kuphedwa. Cifukwa cakuti Mordekai ali ndi udindo waukulu tsopano, anthu ambili athandiza Aisiraeli, ndipo apulumuka kwa adani ao.

Buku la Estere 1-10.