Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 84

Mngelo Afikira Mariya

Mngelo Afikira Mariya

MKAZI wokongola’yo ndi Mariya. Iye ndi Muisrayeli, amene akukhala m’tauni ya Nazarete. Mulungu akudziwa kuti iye ndi munthu wabwino kwambiri. Ndicho chifukwa chake anatumiza mngelo wake Gabrieli kukalankhula naye. Kodi mukudziwa zimene Gabrieli wadza kudzauza Mariya? Tiyeni tione.

‘Moni, woyanjidwa’we,’ akutero Gabrieli kwa iye. ‘Yehova ali nawe.’ Mariya sanaonepo munthu’yu kale. Akubvutika maganizo, chifukwa chakuti sakudziwa chimene akutanthauza. Koma pa nthawi yomwe’yo Gabrieli akum’chotsera mantha ake.

‘Usaope, Mariya,’ iye akutero. ‘Yehova akukondwera nawe kwambiri. N’chifukwa chake adzachita chinthu chodabwitsa kwa iwe. Posakhalitsa udzakhala ndi mwana. Ndipo udzam’cha Yesu.’

Gabrieli akupitiriza kulongosola kuti: ‘Uyu adzakhala wamkulu, ndipo adzachedwa Mwana wa Mulungu Wam’mwamba-mwamba. Yehova adzam’panga kukhala mfumu, monga momwe analiri Davide. Koma iye adzakhala mfumu kosatha, ndipo ufumu wake sudzatha!’

‘Kodi izi zidzachitika bwanji?’ akufunsa motero Mariya. Ndiri wosakwatiwa. Sindinakhale ndi mwamuna, nanga ndingakhale ndi mwana motani?’

‘Mphamvu ya Mulungu idzadza pa iwe,’ akuyankha motero Gabrieli. ‘Chotero mwana’yo adachedwa Mwana wa Mulungu.’ Ndiyeno akuuza Mariya kuti: ‘Kumbukira wachibale wako Elizabeti. Anthu anali kunena kuti anali wokalamba kwambiri kosati n’kukhala ndi ana. Koma posachedwapa adzakhala ndi mwana wamwamuna. Chotero ukuonatu, palibe chosatheka ndi Mulungu.’

Pomwepo Mariya akuti: ‘Ine ndine mdzakazi wa Yehova! Zichitike kwa ine monga momwe mwanenera.’ Pamanepo mngelo’yo akuchoka.

Mariya akufulumira kumka kukazonda Elizabeti. Pamene Elizabeti akumva mau a Mariya, mwana wokhala m’mimba mwa Elizabeti akulumpha mosangalala. Elizabeti akudzazidwa ndi mzimu wa Mulungu, ndipo akuti kwa Mariya: Ndiwe wodala pakati pa akazi onse.’ Mariya akukhala ndi Elizabeti kwa miyezi itatu, ndipo kenako akubwerera kwao ku Nazarete.

Mariya watsala pang’ono kukwatiwa ndi mwamuna wochedwa Yosefe. Koma pamene Yosefe akumva kuti Mariya adzakhala ndi mwana, sakuganiza kuti ayenera kum’kwatira. Ndiyeno mngelo wa Mulungu akulankhula naye kuti: ‘Usaope kutenga Mariya kukhala mkazi wako. Pakuti ndiye Mulungu amene wam’patsa mwana wamwamuna’yo.’ Chotero Mariya ndi Yosefe akukwatirana, ndipo akuyembekezera kubadwa kwa Yesu.