Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 89

Yesu Ayeletsa Kacisi

Yesu Ayeletsa Kacisi

YESU aoneka wokalipa kwambili pacithunzi-thunzi apa, si conco? Nanga udziŵa cifukwa cake iye wakalipa conco? N’cifukwa cakuti amuna awa amene ali pa kacisi wa Mulungu mu Yerusalemu ni aumbombo kwambili. Iwo afuna kupeza ndalama zambili kwa anthu amene abwela pakacisi kudzalambila Mulungu.

Kodi waziona ng’ombe, nkhosa ndi nkhunda? Amuna amenewa agulitsila nyama zimenezi mkati mwa kacisi. Kodi udziŵa cifukwa cake? N’cifukwa cakuti Aisiraeli afunika nyama ndi mbalame zimene angapeleke nsembe kwa Mulungu.

Lamulo la Mulungu linanena kuti ngati Mwisiraeli alakwa, ayenela kupeleka nsembe kwa Mulungu. Ndipo panalinso nthawi zina pamene Aisiraeli anafunikila kupeleka nsembe. Koma kodi Mwisiraeli akanacotsa kuti mbalame ndi nyama zakuti apeleke nsembe kwa Mulungu?

Aisiraeli ena anali kuweta mbalame ndi nyama, ndipo ndiye zimene anali kupeleka nsembe. Koma Aisiraeli ambili analibe nyama kapena mbalame zilizonse. Ndipo ena anali kukhala kutali kwambili ndi Yerusalemu, cakuti kunali kovuta kuti abweletse nyama zao ku kacisi. Conco, anali kubwela ku kacisi kumeneku ndi kugula nyama kapena mbalame zimene anali kufuna. Koma ogulitsa anali kuika mtengo wapamwamba kwambili. Iwo anali kubela anthu. Kuonjezela pamenepo, io sanafunikile kugulitsila mkati mwa kacisi wa Mulungu.

Izi n’zimene zakwiyitsa Yesu. Conco agubuduza mathebulo a osintha ndalama ndi kumwaza ndalama zao. Ndiponso, apanga mkwapulo wanthambo ndi kuthamangitsa nyama zonse zili mu kacisi. Ndiyeno auza anthu ogulitsa nkhunda kuti: ‘Cotsani izi muno! Mulekeletu kusandutsa nyumba ya atate wanga kukhala nyumba ya malonda.’

Ophunzila a Yesu ena ali pamodzi naye pakacisi pamenepo mu Yerusalemu. Iwo adabwa kuona zimene Yesu acita. Ndiyeno akumbukila lemba la m’Baibo limene likamba za Mwana wa Mulungu kuti: ‘Cikondi ca panyumba ya Mulungu cidzayaka mwa iye monga moto.’

Pamene Yesu ali mu Yerusalemu pa cikondwelelo ca Paska, acita zozizwitsa zambili. Pambuyo pake, Yesu acoka ku Yudeya ndi kuyamba ulendo wobwelela ku Galileya. Koma paulendo wobwelela umenewu, apitila m’cigao ca Samariya. Tiye tione zimene zicitika kumeneko.

Yohane 2:13-25; 4:3, 4.