Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 92

Yesu Aukitsa Akufa

Yesu Aukitsa Akufa

MTSIKANA amene uona pacithunzi-thunzi apa ana zaka 12. Yesu agwila dzanja la mtsikanayu ndipo amai ndi atate ake aima pafupi naye. Kodi udziŵa cifukwa cake io aoneka okondwela? Tiye tione cifukwa cake.

Atate a mtsikanayu ni munthu wochuka, ndipo dzina lao ni Yairo. Tsiku lina mwana wao mkazi anadwala kwambili, cakuti anali cabe gone pabedi. Ndipo matenda ake anali kukulila-kulila. Yairo ndi mkazi wake ali ndi nkhawa kwambili, cifukwa cioneka kuti mwana wao adzamwalila. Ndiye mwana mkazi yekha amene ali naye. Conco Yairo ayenda kukafuna-funa Yesu. Anamva za zozizwitsa zimene Yesu acita.

Pamene Yairo apeza Yesu, apeza kuti ali pakati pa anthu ambili. Koma Yairo aloŵa pa gulu la anthu mpaka kufika pamene pali Yesu, ndi kugwada pa mapazi ake. Ndipo auza Yesu kuti: ‘Mwana wanga ni wodwala kwambili. Conde, tiyeni mukamucilitse.’ Yesu amuuza kuti adzapita.

Pamene Yesu ayenda m’njila, anthu akankhana-kankhana kuti aziyenda pafupi naye. Mwadzidzidzi Yesu aima ndi kufunsa kuti: ‘Ndani wanigwila?’ Yesu wamva kuti mphamvu yacoka mwa iye, conco adziŵa kuti pali wina wake amene wamugwila. Koma kodi ndani wamugwila? Ni mkazi wina amene wakhala akudwala kwambili kwa zaka 12. Pamene iye wabwela, wagwila covala ca Yesu ndipo wacila!

Cocitika cimeneci cikondweletsa Yairo kwambili, cifukwa waona kuti n’zosavuta kwa Yesu kucilitsa munthu. Tsopano munthu wina wotumidwa afika, ndipo auza Yairo uthenga wakuti: ‘Musiyeni Yesu musamuvutitse. Mwana wanu wamwalila kale.’ Yesu amvela zimene akambitsilana ndipo auza Yairo kuti: ‘Usade nkhawa, mwana wako adzakhala bwino.’

Pamene afika ku nyumba kwa Yairo, apeza anthu alila cifukwa ca cisoni cacikulu cimene ali naco. Koma Yesu awauza kuti: ‘Osalila, mwana sanamwalile koma ali gone cabe.’ Iwo ayamba kumuseka monyodola, cifukwa adziŵa kuti mwana wamwalila.

Pamenepo Yesu atenga amai ndi atate a mwanayo, ndi atumwi ake atatu, ndi kuloŵa nao m’cipinda mmene mwanayo anali. Iye amugwila dzanja ndi kunena kuti: ‘Uka!’ Ndipo akhala wamoyo, monga mmene uonela pacithunzi-thunzi apa. Mwanayu anyamuka ndi kuyamba kuyenda! Ndiye cifukwa cake amai ndi atate ake ni okondwela kwambili.

Uyu si munthu woyamba amene Yesu wamuukitsa. Woyamba kuukitsa amene Baibo imafotokoza ni mwana wa mkazi wamasiye amene akhala mu mzinda wa Naini. Panthawi ina, Yesu anaukitsanso Lazaro, mlongosi wa Mariya ndi Marita. Pamene Yesu mfumu yosankhidwa ndi Mulungu adzayamba kulamulila, adzaukitsa anthu akufa ambili. Kodi zimenezi si zokondweletsa?

Luka 8:40-56; 7:11-17; Yoh. 11:17-44.