Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 93

Yesu Adyetsa Khamu

Yesu Adyetsa Khamu

KANTHU kena koopsya kachitika. Yohane M’batizi wangophedwa kumene. Herodiya, mkazi wa mfumu, sanam’konde. Ndipo anakhoza kuchititsa mfumu kudula mutu wa Yohane.

Pamene Yesu akumva za izi, akumva chisoni kwambiri. Iye akumka ku malo a yekha. Koma anthu akum’tsatira. Poona khamu’lo, akuwamvera chisoni. Chotero akulankhula nawo za ufumu wa Mulungu, ndipo akuchiritsa odwalo ao.

Madzulo amene’wo ophunzira ake akudza kwa iye nati: ‘kwada kale, ndipo kuno n’kumalo akutali, Tumiza anthu kukagula zakudya zao m’midzi yapafupi.’

Yesu akuyankha kuti, ‘Iwo satofunikira kuchoka. ‘Apatseni kanthu kena kakudya.’ Potembenukira kwa Filipo, Yesu akufunsa kuti: ‘Kodi tikagula kuti chakudya chokwanira kudyetsa anthu onse’wa?’

‘Kukaonongetsa ndalama zochuluka kwambiri kugula chakudya chokwanira kuti ali yense adye pang’ono chabe,’ akuyankha motero Filipo. Andreya akulankhula kuti: ‘Mnyamata’yu, amene akunyamula chakudya chathu, ali ndi mitanda inai ya mikate ndi nsomba ziwiri. Koma sizikwanira konse anthu onse’wa.’

‘Uzani anthu’wo kukhala pansi pa udzu,’ akutero Yesu. Pamenepo iye akuyamika Mulungu kaamba ka chakudya’cho, nayamba kunyema-nyema. Kenako, ophunzira’wo akupatsa anthu onse’wo mkate ndi nsomba. Pali amuna 5,000, ndi akazi ndi ana zikwi zochuluka. Iwo onse akudya mpaka kukhuta. Ndipo pamene ophunzira’wo akusonkhanitsa makombo, pali mitanga 12 yodzadza!

Yesu tsopano akuchititsa ohunizira ake kulowa m’bwato kuoloka Nyanja ya Galileya. M’kati mwa usiku’wo mkuntho waukulu, ndi mapfunde akuchititsa bwatolo kuyenda peyu-peyu. Ophunzira’wo akuchita mantha kwambiri. Ndiyeno, pakati pa usiku, iwo akuona wina wake akuyenda kudza kwa iwo pa madzi. Iwo akupfuula mwamantha, chifukwa chakuti sakudziwa chimene iwo akuona.

Yesu akuti, ‘Musaope. Ndine!’ Iwo sakuzikhulupirirabe. Chotero Petro akuti: ‘Ngati muli inu’di, Ambuye, ndiuzeni kuyenda kudza kuli inu’ko pa madzi.’ Yesu akuyankha kuti: ‘Idza!’ Ndipo Petro akunyamuka nayenda pa madzi! Kenako iye akuchita mantha nayamba kumira, koma Yesu akum’pulumutsa.

Pambuyo pake, Yesu kachiwiri’nso akudyetsa anthu zikwi zochuluka. Pa nthawi ino iye akutero ndi mitanda isanu ndi iwiri ya mkate ndi tinsomba towerengeka. Ndipo kachiwiri’nso pali zokwanira kaamba ka onse. Kodi si zodabwitsa m’mene Yesu amasamalirira anthu? Pamene iye alamulira monga mfumu ya Mulungu sitidzafunikira kudera nkhawa ndi kanthu kali konse!