Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 96

Yesu Achiritsa Odwala

Yesu Achiritsa Odwala

PAMENE Yesu akuyenda-yenda m’dziko’lo, akuchiritsa odwala. Mbiri ya zozizwitsa’zi ikunenedwa m’midzi ndi m’matauni ozungulirapo. Chotero akudza nawo kwa iye awo amene ali opunduka ndi akhungu ndi ogontha, ndi ena ambiri odwala. Ndipo iye akuwachiritsa onse.

Tsopano papita zaka zoposa zitatu chiyambire pamene Yohane M’batizi anabatiza Yesu. Ndipo Yesu akuuza atumwi ake kuti posakhalitsa adzapita ku Yerusalemu, kumene iye adzaphedwa, ndiyeno n’kuuka kwa akufa. Pa nthawi’yi, Yesu akuchiritsabe odwala.

Tsiku lina Yesu akuphunzitsa pa Sabata. Sabata n’tsiku lopumula kwa Ayuda. Mkazi amene mukumuona pano’yu wakhala akudwala kwambiri. Kwa zaka 18 iye anali wokhota msana, ndipo sankatha kuongoka. Chotero Yesu akuika dzanja lake pa iye, ndipo iye akuyamba kuongoka. Wachiritsidwa!

Izi zikukwiyitsa atsogoleri achipembedzo. ‘Pali masiku asanu ndi limodzi amene ife tiyenera kugwira ntchito,’ mmodzi wa iwo akuuza anthu’wo mopfuula. ‘Amene’wo ndiwo masiku a kuchiritsa, osati pa Sabata!’

Koma Yesu akuyankha kuti: ‘Anthu oipa inu. Ali yense wa inu angamasule bulu wake ndi kum’tulutsa kukamwa madzi pa Sabata. Chotero kodi mkazi wobvutika’yu, amene wakhala chidwalire kwa zaka 18, sayenera kuchiritsidwa pa Sabata?’ Yankho la Yesu likuchititsa manyazi anthu oipa’wa.

Kenako Yesu ndi atumwi ake akuyenda kumka ku Yerusalemu. Atafika kunja kwa tauni ya Yeriko, akhungu awiri opemphapempha akumva kuti Yesu adzapita pemenepo. Chotero iwo akupfuula kuti: ‘Yesu, tithandizeni!’

Yesu akuitana akhungu’wo nawafunsa kuti: ‘Kodi mufuna ndikuchitireni chiani?’ Iwo akuti: ‘Ambuye, tsegulani maso athu.’ Yesu akukhudza maso ao, ndipo pomwepo iwo akutha kuona! Kodi mukudziwa chifukwa chake Yesu akuchita zozizwitsa zonse’zi? Chifukwa chakuti amakonda anthu ndipo amafuna kuti am’khulupirire. Ndipo chotero tingakhale otsimikizira kuti pamene iye alamulira monga Mfumu palibe ali yense pa dziko lapansi adzadwala’nso.