Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 96

Yesu Acilitsa Odwala

Yesu Acilitsa Odwala

PAMENE Yesu ayenda-yenda mu dziko lonse, acilitsanso odwala. Mbili ya zozizwitsa zimenezi ifalikila m’midzi ndi m’mizinda yonse. Conco anthu abweletsa kwa Yesu anthu olemala, osaona, osamva ndi anthu ena ambili amene adwala. Ndipo Yesu awacilitsa onse.

Papita zaka zoposa zitatu tsopano kucokela pamene Yohane anabatiza Yesu. Ndiyeno Yesu auza atumwi ake kuti iye adzapita ku Yerusalemu, ndipo kumeneko adzaphedwa, komabe adzaukitsidwa ku imfa. Koma Yesu apitiliza kucilitsa odwala.

Tsiku lina Yesu anali kuphunzitsa pa Sabata. Sabata ni tsiku lopumula la Ayuda. Mkazi amene uona pacithunzi-thunzi apa wakhala akudwala kwambili. Kwa zaka 18 anali ndi msana wopindika cakuti sanali kukwanitsa kuwelamuka. Conco Yesu aika manja pa iye ndipo ayamba kuwelamuka. Pamenepo iye acila!

Zocitika zimenezi zipangitsa atsogoleli acipembedzo kukalipa. Mmodzi wa io afuula ku gulu la anthu kuti: ‘Pali masiku 6 oyenela kugwila nchito. Muzibwela masiku amenewo kudzacilitsidwa, osati tsiku la Sabata!’

Koma Yesu ayankha kuti: ‘Anthu oipa inu. Aliyense wa inu angamasule bulu wake mu khola pa Sabata ndi kupita naye kukamumwetsa madzi. Kodi sikuli koyenela kuti mkazi uyu, amene wakhala wodwala kwa zaka 18, acilitsidwe pa tsiku la Sabata?’ Yankho la Yesu liwacititsa manyazi amuna oipa awa.

Pambuyo pake, Yesu ndi atumwi ake ayenda ulendo wopita ku Yerusalemu. Pamene afika m’malile a mzinda wa Yeriko, amuna aŵili osaona amvela kuti Yesu apita ca kufupi ndi kumene io ali. Conco ayamba kufuula kuti: ‘Yesu, tithandizeni!’

Yesu aitana amuna osaona ndi kuwafunsa kuti: ‘Mufuna kuti n’kucitileni ciani?’ Iwo akuti: ‘Ambuye, titseguleni maso.’ Yesu agwila maso ao, ndipo nthawi imeneyo ayamba kuona! Kodi udziŵa cifukwa cake Yesu acita zozizwitsa zimenezi? N’cifukwa cakuti amakonda anthu, ndipo afuna kuti io akhale ndi cikhulupililo mwa iye. Conco ndife otsimikiza kuti nthawi imene adzalamulila monga Mfumu, sipadzakhalanso odwala padziko lapansi.