Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 97

Yesu Abwela Monga Mfumu

Yesu Abwela Monga Mfumu

PATAPITA kanthawi kucokela pamene Yesu anacilitsa anthu osana aŵili opempha-pempha, abwela ku mudzi waung’ono umene uli pafupi ndi Yerusalemu. Kumeneko auza ophunzila ake aŵili kuti: ‘Pitani m’mudzi ndipo mudzapeza bulu wamng’ono. Mum’masule ndipo mum’bweletse kwa ine.’

Pamene abweletsa bulu kwa iye, Yesu akwelapo. Ndiyeno apita ku Yerusalemu mzinda umene uli capafupi. Pamene afika pafupi ndi mzinda umenewu, khamu la anthu libwela kudzamulandila. Anthu ambili avula malaya ao ovala pamwamba ndi kuwayala pamseu. Ena adula masamba a mtengo wa kanjedza ndi kuwayala pamseu, ndipo afuula kuti: ‘Mulungu adalitse mfumu yobwela mu dzina la Yehova!’

Kale mu Isiraeli, mafumu atsopano anali kuloŵa mu Yerusalemu atakwela pa bulu wamng’ono kuti aonekele kwa anthu. Izi ndiye zimene Yesu acita. Ndipo anthu awa aonetsa kuti afuna Yesu kuti akhale mfumu yao. Koma si anthu onse amene amufuna. Tidziŵa zimenezi cifukwa ca zimene zicitika pamene Yesu ayenda ku kacisi.

Pamene Yesu ali pa kacisi, acilitsa anthu osaona ndi olemala. Ana ang’ono ataona zimenezi, afuula kutamanda Yesu. Koma zimenezi zikwiyitsa ansembe, ndipo auza Yesu kuti: ‘Kodi umvela zimene ana awa akamba?’

Yesu awayankha kuti: ‘Inde, kodi simunaŵelenge m’Baibo pamene imati: “M’kamwa mwa ana ang’ono Mulungu aikamo mau otamanda?’’’ Conco ana apitiliza kutamanda mfumu yosankhidwa ndi Mulungu.

Tifuna kukhala monga ana amenewo, si conco? Anthu ena angatiletse kukamba za ufumu wa Mulungu. Koma tifunika kupitiliza kuuza ena zinthu zabwino zimene Yesu adzacitila anthu.

Pamene Yesu anali padziko lapansi, siinali nthawi yake yakuti ayambe kulamulila monga mfumu. Nanga nthawi imeneyi idzafika liti? Ophunzila a Yesu afuna kudziŵa. Tidzaphunzila zimenezi m’nkhani yotsatila.

Mateyu 21:1-17; Yohane 12:12-16.