Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 98

Pa Phili La Maolivi

Pa Phili La Maolivi

UYU ni Yesu ali pa Phili la Maolivi. Amuna anai amene ali nao ni atumwi ake. Andreya ndi Petulo ali pacibale, ndiponso Yakobo ndi Yohane naonso ali pacibale. Cimene uona capatali apo ni kacisi wa Mulungu ku Yerusalemu.

Papita masiku aŵili kucokela pamene Yesu analoŵa mu Yerusalemu atakwela pa bulu wamng’ono, ndipo tsikuli ni pa Ciŵili. Kuciyambi kwa tsikuli Yesu anali pakacisi. Ali kumeneko, ansembe ayesa kumugwila kuti amuphe. Koma acita mantha cifukwa cakuti anthu amamukonda Yesu.

Yesu anauza atsogoleli acipembedzo kuti, ‘Inu njoka ndi ana a njoka!’ Anawauzanso kuti Mulungu adzawalanga cifukwa ca zoipa zonse zimene anacita. Pambuyo pake Yesu anakwela m’phili la maolivi. Ndiyeno atumwi anai amenewa ayamba kumufunsa mafunso. Kodi udziŵa zimene io afunsa Yesu?

Atumwiwo amufunsa zinthu za kutsogolo. Adziŵa kuti Yesu adzacotsa zoipa zonse padziko lapansi. Koma afuna kudziŵa kuti zimenezi zidzacitika liti. Kodi ndi liti pamene Yesu adzabwelanso kudzalamulila monga Mfumu?

Yesu adziŵa kuti otsatila ake a padziko lapansi sadzamuona pamene adzabwelanso. N’cifukwa cakuti iye adzakhala kumwamba, ndipo io sangamuone ali kumeneko. Conco, Yesu auza atumwi ake zinthu zina zimene zidzayamba kucitika padziko lapansi, pamene adzayamba kulamulila monga Mfumu kumwamba. Kodi n’zinthu ziti zimenezo?

Yesu akuti padzakhala nkhondo zazikulu, anthu ambili adzakhala ndi matenda ndi njala, upandu udzafalikila, ndiyeno padzakhala zivomezi zazikulu. Yesu anakambanso kuti uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu udzalalikidwa padziko lonse lapansi. Kodi zinthu zimenezi zimacitika zoona masiku ano? Inde! Conco tingatsimikize kuti Yesu tsopano alamulila kumwamba. Posacedwapa, adzacotsa zoipa zonse padziko lapansi.