Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 99

M’cipinda Capamwamba

M’cipinda Capamwamba

MASIKU aŵili apitapo, tsopano n’pa Cinai nthawi yausiku. Yesu ndi atumwi ake 12 abwela m’cipinda capamwamba ici kuti acite Paska. Mwamuna amene acoka uyo ni Yudasi Isikariyoti. Apa m’pamene ayenda kukauza ansembe mmene angagwilile Yesu.

Kutatsala tsiku limodzi kuti acite Paska, Yudasi anayenda kwa io kukawafunsa kuti: ‘Kodi mudzanipatsa ciani nikakuthandizani kugwila Yesu?’ Iwo anati: ‘Ndalama 30 zasiliva.’ Conco Yudasi tsopano ayenda kukumana ndi amuna amenewa kuti awapeleke kumene kuli Yesu. Cimeneci ni cinthu coipa kwambili, si conco?

Paska yatha, koma Yesu tsopano ayamba phwando lina lapadela. Apeleka mkate kwa atumwi ake ndi kuwauza kuti: ‘Idyani cifukwa mkate uwu uimila thupi langa limene lidzapelekedwa kaamba ka inu.’ Ndiyeno awapatsa kapu ya vinyo ndi kuwauza kuti: ‘Imwani, vinyo ameneyu aimila magazi anga amene adzakhetsedwa kaamba ka inu.’ Baibo imacha phwando limeneli kuti ‘Mgonelo wa Ambuye,’ kapena Cakudya Camadzulo ca Ambuye.’

Aisiraeli anali kucita Paska pokumbukila nthawi imene mngelo wa Mulungu ‘anapitilila’ nyumba zao mu Iguputo, koma anapha ana oyamba mu nyumba za Aiguputo. Koma tsopano Yesu afuna kuti otsatila ake azimukumbukila, komanso kuti azikumbukila mmene anapelekela moyo wake kaamba ka io. Ndipo n’cifukwa cake awauza kuti azicita phwando lapadela limeneli caka ciliconse.

Pamene anatsiliza kucita Mgonelo wa Ambuye, Yesu auza atumwi ake kuti afunika kukhala olimba mtima ndi okhulupilika kwambili. Potsilizila pake, aimba nyimbo zotamanda Mulungu ndi kucoka pamalowo. Tsopano ni nthawi yausiku kwambili, mwinamwake kupitilila pakati pausiku. Tiye tione kumene io ayenda.

Mateyu 26:14-30; Luka 22:1-39; Yohane caputa 13 mpaka 17; 1 Akorinto 11:20.