Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 103

Akulowa m’Chipinda Chotseka

Akulowa m’Chipinda Chotseka

PETRO ndi Yohane atachoka pa manda amene mtembo wa Yesu unali, Mariya akutsalapo yekha. Akuyamba kulira. Ndiyeno akuwerama nasuzumiramo, monga momwe tinaonera m’chithunzi chotsirizira. Akuonamo angelo awiri! Iwo akum’funsa kuti: ‘Ukuliriranji?’

Iye akuyankha kuti: ‘Atenga Mbuyanga, sindidziwa kuti amuika kuti.’ Mariya akutembenukano ndipo akuona mwamuna. Akum’funsa kuti: ‘Kodi ukufuna-funa yani?’

Mariya akuganiza kuti munthu’yo ndi wolima m’munda, ndi kuti iye angakhale atatenga mtembo wa Yesu. Chotero akuti: ‘Ngati mwam’tenga, ndiuzeni kumene mwamuika.’ Koma, kweni-kweni, mwamuna’yu ndi Yesu. Iye wabvala thupi limene Mariya sakulidziwa. Koma atamuitana dzina lake, iye akudziwa kuti ndi Yesu. Iye akuthamanga nauza ophunzira ake kuti: ‘Ndaona Ambuye!’

Nthawi ina pa tsiku’lo, ophunzira awiri akuyenda kumka ku mudzi wa Emau, mwamuna wina akutsagana nawo. Ophunzira’wo ali achisoni kwambiri chifukwa chakuti Yesu waphedwa. Koma pamene akuyenda, munthu’yo akulongosola zambiri zochokera m’Baibulo zimene zikuwapangitsa kumva bwino kwambiri. Kenako, poima kuti adye, iwo akudziwa kuti munthu’yu ndi Yesu. Ndiyeno iye akuzimiririka, ndipo ophunzira’wo akubwerera ku Yerusalemu mofulumira kukauza atumwi za iye.

Pamene izi zikuchitika, Yesu akuonekera’nso pa Petro. Enawo akuchita nthumanzi pomva izi. Ndiyeno ophunzira awiri’wa akumka ku Yerusalemu napeza atumwi. Akuwauza m’mene Yesu anaonekerera kwa iwo’nso pa mseu. Akali chisimbire izi, kodi mukudziwa chodabwitsa chimene chikuchitika?

Taonani pa chithunzi’cho. Yesu akuonekera m’chipindamo, ngakhale chitseko chiri chotseka. Ha, ophunzira’wo ndi okondwa chotani nanga! Kodi limene’lo si tsiku la chisangalalo? Kodi mungawerenge kuti Yesu waonekera kwa atsatiri ake kangati tsopano? Kodi kakwana kasanu?

Mtumwi Tomasi sali nawo pamene Yesu akuonekera. Chotero ophunzira’wo akumuuza kuti: ‘Taona Ambuye!’ Koma Tomasi akuti adzafunikira kuona yekha Yesu kuti akhulupirire. Eya, patapita masiku asanu ndi atatu ophunzira’wo ali pamodzi’nso m’chipinda chotsekedwa, pa nthawi’yi Tomasi ali nawo. Mwadzidzidzi, Yesu akuonekera m’chipindamo. Tsopano Tomasi akukhulupirira.