Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 104

Yesu Abwelela Kumwamba

Yesu Abwelela Kumwamba

M’KUPITA kwa masiku, Yesu aonekela kwa otsatila ake nthawi zambili. Panthawi ina aonekela kwa ophunzila ake 500. Pamene aonekela kwa io, kodi udziŵa zimene Yesu awauza? Awauza za ufumu wa Mulungu. Yehova anatumiza Yesu padziko lapansi kuti adzaphunzitse anthu za Ufumu. Ndipo apitiliza kucita zimenezi ngakhale pambuyo poukitsidwa ku imfa.

Kodi ukumbukila kuti ufumu wa Mulungu n’ciani? Ufumuwu ni boma leni-leni la Mulungu la kumwamba, ndipo Yesu ndiye amene Mulungu anasankha kukhala mfumu. Monga mmene tinaphunzilila, Yesu anaonetsa kuti adzakhala mfumu yabwino kwambili pamene anadyetsa anthu anjala, anacilitsa odwala ndiponso pamene anaukitsa akufa.

Conco pamene Yesu adzalamulila monga mfumu kumwamba kwa zaka 1000, kodi zinthu padziko lapansi zidzakhala bwanji? Dziko lonse lapansi lidzakhala paladaiso yabwino kwambili. Sikudzakhala nkhondo, upandu, kudwala ngakhale imfa. Tidziŵa kuti zimenezi n’zoona cifukwa Mulungu anapanga dziko lapansi kuti likhale paladaiso yokhalamo anthu. Ndiye cifukwa cake paciyambi anapanga munda wa Edeni. Ndipo Yesu adzatsimikizila kuti zimene Mulungu afuna kuti zicitike zacitika.

Nthawi tsopano ifika yakuti Yesu abwelele kumwamba. Kwa masiku 40, Yesu aonekela kwa ophunzila ake. Conco io atsimikizila kuti iye wakhalanso moyo. Koma Yesu akalibe kusiyana ndi ophunzila ake, awauza kuti: ‘Musatuluke mu Yerusalemu mpaka mutalandila mzimu woyela.’ Mzimu woyela ndi mphamvu ya Mulungu yogwila nchito, monga mphepo imene imaomba. Mzimu umenewu udzathandiza otsatila ake kucita cifunilo ca Mulungu. Potsilizila pake, Yesu akuti: ‘Muyenela kulalikila za ine kufikila kumalekezelo a dziko lapansi.’

Pambuyo pokamba mau amenewa, cinthu codabwitsa cicitika. Yesu ayamba kupita kumwamba monga mmene uonela pacithunzi-thunzi apa. Ndiyeno mtambo umubisa, ndipo ophunzila ake samuonanso. Yesu apita kumwamba, ndipo ayamba kulamulila otsatila ake kucokela kumwamba.

1 Akorinto 15:3-8; Chivumbulutso 21:3, 4; Machitidwe 1:1-11.