Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 105

Ayembekezela Mu Yerusalemu

Ayembekezela Mu Yerusalemu

ANTHU amene ali pacithunzi-thunzi apa ni otsatila a Yesu. Anatsatila zimene iye anawauza ndipo sanacoke mu Yerusalemu. Ndipo pamene onse ayembekezela, mwadzidzidzi anayamba kumvela congo kwambili. Congo cimeneci cimveka monga cimphepo camphamvu. Ndiyeno moto wooneka monga malilime unayamba kuonekela pamutu pa wophunzila aliyense. Kodi wauona moto umene uli pamutu pa aliyense? Kodi zonsezi zitanthauza ciani?

Cimeneci ni cozizwitsa! Yesu ali kumwamba ndi Atate ake, koma tsopano atumiza mzimu woyela wa Mulungu kwa otsatila ake. Kodi udziŵa cimene mzimu umenewu uwapangitsa kucita? Onse ayamba kukamba zinenelo zosiyana-siyana.

Anthu ambili mu Yerusalemu amvela za congo cimene cili monga cimphepo camphamvu, ndipo abwela kuti adzaone zimene zicitika. Ena mwa anthu amenewa ni a mitundu ina ndipo abwela kuphwando la Aisiraeli la Pentekoste. Alendo amenewa adabwa kwambili! Iwo amvela ophunzila akamba mu zinenelo zao zinthu zodabwitsa zimene Mulungu acita.

Alendowo akuti: ‘Kodi onse amene akamba awa si Agalileya? Nanga zatheka bwanji kuti io akambe zinenelo zosiyana-siyana za kumaiko amene ticokela ife?’

Ndiyeno Petulo anyamuka kuti awafotokozele. Iye akamba mokweza mau ndi kuuza anthu mmene Yesu anafela, ndi kuti Yehova anamuukitsa kwa akufa. Petulo akuti: ‘Tsopano Yesu ali kumwamba kudzanja lamanja la Mulungu. Ndipo watiponyela mzimu woyela umene anatilonjeza. N’cifukwa cake mwaona ndi kumva zozizwitsa izi.’

Pamene Petulo akamba zinthu izi, anthu ambili amvela cisoni kwambili pa zimene zinacitikila Yesu. Iwo afunsa kuti: ‘Kodi ife tidzacita ciani pamenepa? Petulo awauza kuti: ‘Muyenela kusintha makhalidwe anu kuti mubatizike.’ Conco patsiku limenelo anthu pafupi-fupi 3,000 abatizika, ndipo akhala otsatila a Yesu.

Machitidwe 2:1-47.