Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 106

Amasulidwa m’Ndende

Amasulidwa m’Ndende

TAONANI mngelo watsegula chitseko cha ndende’yu pano. Amuna amene akuwamasula’wo ndiwo atumwi a Yesu. Tiyeni tione chimene chinachititsa kumangidwa kwao m’ndende.

Pangopita kanthawi chiyambire pamene mzimu woyera unatsanuliridwa pa ophunzira a Yesu. Ndipo nazi zimene zikuchitika: Petro ndi Yohane akulowa m’kachisi mu Yerusalemu masana. Kumene’ko pafupi ndi chitseko, pali munthu wopunduka chibadwire. Anthu amam’nyamula kudza naye pano tsiku liri lonse kuti adzapemphe ndalama kwa awo olowa m’kachisi. Poona Petro ndi Yohane, akuwapempha kum’patsa kanthu kena. Kodi atumwi’wo adzachitanji?

Iwo akuima nayan’gana munthu wobvutika’yo. Petro anati, ‘Ndiribe ndalama, koma ndidzakupatsa chimene ndiri nacho. M’dzina la Yesu, nyamuka nuyende!’ Ndiyeno Petro akugwira dzanja lamanja munthu’yo, pompo akulumpha nayamba kuyenda. Anthu poona izi, akudabwa ndi kukondwa kwambiri ndi chozizwitsa chodabwitsa’chi.

Petro akuti: ‘Ndi mwa mphamvu ya Mulungu, amene anaukitsa Yesu kwa akufa, kuti tinachita chozizwitsa’chi.’ Iye ndi Yohane akali chilankhulire, atsogoleri ena achipembedzo akudza. Iwo aipidwa chifukwa chakuti Petro ndi Yohane akuuza anthu za Yesu kuti anaukitsidwa. Chotero akuwagwira nawaika m’ndende.

M’mawa mwake atsogoleri achipembedzo’wo akuchita chimsonkhano. Petro ndi Yohane, limodzi ndi wochiritsidwa’yo akulowetsedwamo. Atsogoleri achipembedzo’wo akufunsa kuti, ‘Kodi munachita chozizwitsa’chi m’mphamvu ya yani?’

Petro akuwauza kuti mwa mphamvu ya Mulungu, amene anaukitsa Yesu. Ansembe sakudziwa chochita, pakuti sangakane kuti chozizwitsa’chi chinachitika’di. Chotero iwo akuchenjeza atumwi kusalankhula’nso za Yesu, nawalola kupita.

Pamene masiku akupita iwo akulalikira za Yesu ndi kuchiritsa odwala. Mbiri ya zozizwitsa’zi ikufalikira. Chotero ngakhale makamu ochokera ku matauni apafupi ndi Yerusalemu akudza ndi odwala kuti atumwi adzawachiritse. Izi zikuchititsa nsanje atsogoleri achipembedzo, chotero akugwira atumwi’wo nawaika m’ndende. Koma sakukhalamo kwa nthawi yaitali.

Usiku mngelo wa Mulungu akutsegula chitseko cha ndende, monga momwe mukuonera pano. Iye akuti: ‘Mukani mukaime m’kachisi, ndi kupitiriza kulankhula ndi anthu’wo.’ M’mawa mwake, pamene atsogoleri achipembedzo’wo atumiza anthu ku ndende kukatenga atumwi, mulibe. Pambuyo pake amuna’wo akuwapeza akuphunzitsa m’kachisi nadza nawo ku holo ya Sanhedrini.

Atsogoleri achipembedzo’wo akuti: ‘Tinakulamulirani mwamphamvu kuti musaphumzitse’nso za Yesu. Onani inu mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu.’ Atumwi’wo akuyankha kuti: ‘Tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira koposa anthu.’ Chotero iwo akupitirizabe kuphunzitsa “mbiri yabwino.” Kodi icho si chitsanzo chabwino kwa ife kuti tichitsatire?