Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 106

Awacotsa M’ndende

Awacotsa M’ndende

ONA mngelo pacithunzi-thunzi apa amene watsegula citseko ca ndende. Amuna awa amene acotsedwa m’ndende ni atumwi a Yesu. Tiye tione cimene cinapangitsa kuti awaponye m’ndende.

Papita nthawi yocepa cabe kucokela pamene mzimu woyela unabwela pa ophunzila a Yesu. Ndipo zimene zicitika ni izi: Tsiku lina nthawi ya kumasana, Petulo ndi Yohane aloŵa mu kacisi ku Yerusalemu. Pafupi ndi citseko pali munthu amene ni wolemala cibadwile. Masiku onse anthu amamunyamula ndi kumupeleka pakhomo la kacisi kuti azipempha ndalama kwa anthu amene amaloŵa mu kacisi. Pamene iye aona Petulo ndi Yohane, awapempha kuti amupatseko ndalama. Kodi atumwi adzacita ciani?

Iwo aimilila ndi kuyang’ana munthu wolemala ameneyu. Petulo akuti: ‘Ndilibe ndalama, koma ndikupatsa cimene ndili naco. M’dzina la Yesu nyamuka ndi kuyenda!’ Ndiyeno Petulo amugwila dzanja lamanja, ndipo nthawi imeneyo munthuyo alumpha m’mwamba ndi kuyamba kuyenda. Pamene anthu aona zimenezi, adabwa kwambili ndipo akondwela kwambili cifukwa ca cozizwitsa cimeneci.

Petulo akuti: ‘Tacita cozizwitsa ici mwa mphamvu ya Mulungu amene anaukitsa Yesu kwa akufa.’ Pamene iye ndi Yohane akali kulankhula, atsogoleli acipembedzo abwela. Iwo akwiya kwambili cifukwa cakuti Petulo ndi Yohane auza anthu za kuukitsidwa kwa Yesu. Conco awagwila ndi kuwaponya mu ndende.

Tsiku lotsatila, atsogoleli acipembedzo akhala ndi msonkhano waukulu. Petulo ndi Yohane, pamodzi ndi munthu amene io anacilitsa awabweletsa pamsonkhano umenewu. Atsogoleli acipembedzo afunsa kuti: ‘Kodi unacita cozizwitsa ici mwa mphamvu ya ndani?’

Petulo awauza kuti ndi mwa mphamvu ya Mulungu amene anaukitsa Yesu kwa akufa. Ansembe sadziŵa zocita, cifukwa sangatsutse kuti cozizwitsa cimeneci sicinacitike. Conco acenjeza atumwi kuti asalankhulenso za Yesu, ndiyeno awalamula kuti apite.

M’kupita kwa nthawi, atumwi apitiliza kulalikila za Yesu ndi kucilitsa odwala. Mbili yonena za zozizwitsa zimenezi ifalikila. Conco ngakhale anthu ocokela ku mizinda imene ili pafupi ndi Yerusalemu abweletsa anthu odwala kuti atumwi awacilitse. Zimenezi zicititsa atsogoleli acipembedzo kucita nsanje, cakuti io agwila atumwi ndi kuwaponya mu ndende. Koma io sakhalamo nthawi itali.

Nthawi yausiku, mngelo wa Mulungu atsegula citseko ca ndende monga mmene uonela pacithunzi-thunzi apa. Mngeloyo akuti: ‘Pitani, ndipo mukaimilile mu kacisi ndi kupitiliza kuuza anthu.’ Tsiku lotsatila, nthawi ya kum’mawa pamene atsogoleli acipembedzo auza anthu kupita kundende kuti akatenge atumwi, io sawapeza. Nthawi ina anthu apeza atumwi ali mu kacisi aphunzitsa, conco awatenga ndi kuwabweletsa ku khoti yalikulu ya Ayuda

Atsogoleli acipembedzo akuti: ‘Tinakulamulani mwamphamvu kuti musaphunzitsenso za Yesu, koma mwadzaza Yerusalemu yense ndi ciphunzitso canu.’ Ndiyeno atumwi ayankha kuti: ‘Tiyenela kumvela Mulungu monga wolamulila kuposa anthu.’ Conco io apitiliza kulalikila “uthenga wabwino.” Cimeneci ni citsanzo cabwino kwambili cimene ife tiyenela kutsatila.

Machitidwe caputa 3 mpaka 5.