Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 108

Pa Njira ya ku Damasiko

Pa Njira ya ku Damasiko

KODI mukum’dziwa wagona kwala pansi’yo? Ndiye Saulo. Pajatu, ndiye’tu amene anasunga malaya a amuna amene anaponya miyala Stefano. Taonani kuwala konyezimira’ko! Kodi chikuchitika n’chiani?

Stefano ataphedwa, Saulo akutsogolera m’kusaka-saka atsatiri a Yesu kuti awabvulaze. Iye akumka ku nyumba ndi nyumba nawakwakwazira kunja ndi kuwaponya m’ndende. Ophunzira ambiri akuthawira ku mizinda ina nayamba kulengeza “mbiri yabwino” kumene’ko. Koma Saulo akumka ku mizinda ina’yo kukasokolotsa atsatiri a Yesu. Iye tsopano ali pa ulendo womka ku Damasiko. Koma, ali pa njira, ichi ndicho chozizwitsa chimene chikuchitika:

Mwadzidzidzi kuunika kochokera kumwamba kukuwala mozinga Saulo. Iye akugwera pansi, monga momwe tikuonera pano. Ndiyeno mau akuti: ‘Saulo, Saulo! Undilonda-londeranji?’ Amuna okhala ndi Saulo akuona kuwala’ko namva phokoso la mau’wo, koma sakumvetsetsa zonenedwa.

Saulo akufunsa kuti, Ndinu yani, Mbuye?’

Mau’wo akuti, ‘Ndine Yesu, amene um’londa-londa.’ Yesu akunena izi chifukwa chakuti pamene Saulo akubvutitsa atsatiri a Yesu, Yesu amamva ngati kuti iye mwini akubvutitsidwa.

Saulo tsopano akufunsa kuti: ‘Ndichitenji Mbuye?’

Yesu akuti, ‘Nyamuka nulowe m’Damasiko. Kumene’ko udzauzidwa choti uchite.’ Pamene akunyamuka natsegula maso ake, sakuona chinthu. Iye wachita khungu! Chotero amuna okhala naye akum’gwira dzanja kulowa naye m’Damasiko.

Yesu tsopano akulankhula ndi mmodzi wa ophunzira ake m’Damasiko, nati: ‘Tauka, Hananiya. Pita ku khwalala lochedwa Lolunjika. Pa nyumba ya Yuda kafunse za munthu wochedwa Saulo. Ndam’sankha akhale mtumiki wanga wapadera.’

Hananiya akumvera. Pokumana ndi Saulo, akuika manja ake pa iye nati: ‘Ambuye wandituma kwa iwe kuti upenye’nso nudzazidwe ndi mzimu woyera.’ Pomwepo kanthu kena konga mamba kakugwa m’maso a Saulo, ndipo akuona’nso.

Saulo akugwiritsiridwa ntchito mwamphamvu kulalikira anthu ambiri a amitundu. Iye akufikira pa kuchedwa mtumwi Paulo, za amene tidzaphunzira zina zambiri. Koma choyamba, tiyeni tione zimene Mulungu akutumiza Petro kukachita.