Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 109

Petro Achezera Korneliyo

Petro Achezera Korneliyo

UYO ndi mtumwi Petro waima apo’yo, ndipo awo ndi ena a mabwenzi ake ali kumbuyo kwake’wo. Koma kodi mwamuna’yo akugwadiriranji Petro? Kodi iye ayenera kuchita zimene’zo? Kodi mukudziwa kuti iye ndani?

Mwamuna’yo ndiye Korneliyo. Iye ndi mkulu wa gulu la nkhondo Lachiroma. Korneliyo sakudziwa Petro, koma anauzidwa kumuitanira kunyumba kwake. Tiyeni tione m’mene izi zinachitikira.

Atsatiri oyambirira a Yesu anali Ayuda, koma Korneliyo si Myuda. Komabe amakonda Mulungu, amapemphera kwa iye, ndipo amachitira anthu zokoma mtima zambiri. Eya, masana ena mngelo anaonekera kwa iye nati: ‘Mulungu akondwera nawe, ndipo adzayankha mapemphero ako. Tumiza anthu apite kwa munthu wina wochedwa Petro. Akukhala m’Yopa pa nyumba ya Simoni, amene amakhala m’mbali mwa nyanja.’

Pomwepo Korneliyo akutumiza anthu ena kumka kukafuna Petro. M’mawa mwake, pamene anthu’wo akuyandikira ku Yopa, Petro ali pa tsindwi lathyathyathya la nyumba ya Simoni. Pamenepo Mulungu akupangitsa Petro kuganiza kuti akuona chinsalu chikutsika kuchokera kumwamba. M’menemo muli mitundu yonse ya zinyama. Malinga ndi kunena kwa chilamulo cha Mulungu, zinyama zimene’zi zinali zosayenera kudyedwa, ndipo komabe mau akuti: ‘Tauka Petro. Ipha nudye.’

Petro akuti, ‘Ai! chikhalire sindinadye chodetsedwa.’ Koma mau’wo akumuuza kuti: ‘Leka kucha chodetsedwa chimene Mulungu tsopano akuti n’choyera.’ Izi zikuchitika katatu konse. Akali chidabwire chimene zimene’zi zikutanthauza, amuna otumizidwa ndi Korneliyo aja akufika panyumba’po nafunsa za Petro.

Petro akutsika nati: ‘Ine ndine munthu amene mukufuna-funa. Mwadzeranji? Atalongosola amuna’wo kuti mngelo anauza Korneliyo kuitanira Petro ku nyumba kwake, iye akubvomereza kumka nawo. M’mawa mwake iye ndi mabwenzi ake akunyamuka kumka kukachezera Korneliyo m’Kaisareya.

Korneliyo wasonkhanitsa achibale ndi mabwenzi ake onse apamtima. Pofika Petro, iye akum’chingamira. Iye akugwa pansi nagwada pa mapazi a Petro, monga momwe mukuonera pano. Koma Petro akuti: ‘Nyamuka; Ine ndine munthu chabe.’ Inde, Baibulo limasonyeza kuti n’kosayenera kugwadira ndi kulambira munthu. Tiyenera kulambira Yehova.

Petro akulalikirano osankhana’wo. ‘Ndikuona kuti Mulungu amalandira anthu onse amene amafuna kum’tumikira,’ akutero Petro. Akali chilankhulire, Mulungu akutumiza mzimu wake woyera, anthu’wo nayamba kulankhula zinenero zosiyana. Izi zikudabwitsa ophunzira Achiyuda amene adza ndi Petro, chifukwa iwo anaganiza kuti Mulungu amayanja Ayuda okha. Izi zikuwaphunzitsa kuti Mulungu samaona anthu a pfuko liri lonse kukhala abwinopo kapena ofunika kwambiri kwa iye koposa a pfuko lina. Kodi si zabwino kwa ife tonse kuzikumbukira?