Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 109

Petulo Acezela Korneliyo

Petulo Acezela Korneliyo

UYU amene waimilila patsogolo ni mtumwi Petulo, ndipo amene ali kumbuyo kwake ni anzake. Nanga n’cifukwa ciani mwamuna uyu agwadila Petulo? Kodi ayenela kucita zimenezi? Kodi mwamuna ameneyu umudziŵa?

Mwamuna ameneyu ni Korneliyo. Ni msilikali wa Roma. Korneliyo sadziŵana ndi Petulo, koma anauzidwa kuti amuitanile kunyumba kwake. Tiye tione mmene zimenezi zinakhalila conco

Otsatila oyambilila a Yesu anali Ayuda, koma Korneliyo si Myuda. Komabe, iye akonda Mulungu, amapemphela kwa iye ndipo amacitila anthu zinthu zabwino zambili. Koma tsiku lina mngelo anaonekela kwa iye, ndipo akuti: ‘Mulungu wakondwela ndi nchito zako ndipo adzayankha mapemphelo ako. Cotelo, tumiza anthu kuti akaitane munthu wina dzina lake Petulo. Munthu ameneyu akhala ku Yopa kunyumba kwa Simoni, amene nyumba yake ili m’mbali mwa nyanja.’

Nthawi imeneyo, Korneliyo atuma anchito ake kuti akaitane Petulo. Tsiku lotsatila, pamene amunawa ayandikila mzinda wa Yopa, Petulo ali pamtenje wa nyumba ya Simoni. Petulo akali pamtenje, Mulungu amuonetsa m’masomphenya cinsalu cacikulu cimene ciseluka kumwamba. Ndipo pacinsalupo pali nyama za mitundu yonse. Malinga ndi cilamulo ca Mulungu, nyama zonsezi n’zodetsedwa, zosayenela kudya, koma mau akuti: ‘Nyamuka Petulo, ipha udye!’

Petulo ayankha kuti: ‘Iyai! Sin’nadyepo zinthu zodetsedwa.’ Koma mau auza Petulo kuti: ‘Zinthu zimene Mulungu waziyeletsa, uleke kukamba kuti n’zodetsedwa.’ Mau amenewa amveka katatu konse. Pamene Petulo akali kuganizila tanthauzo la zimenezi, amuna amene Korneliyo watuma afika panyumba ndi kufunsa ngati Petulo alipo.

Petulo aseluka pamtenje ndi kukamba kuti: ‘Munthu amene mufuna ndine. Kodi mwabwela kucita ciani?’ Amunawo akamba kuti mngelo anauza Korneliyo kuti aitanile Petulo kunyumba kwake. Petulo avomela kuti adzayenda nao. Tsiku lotsatila, Petulo ndi anzake anyamuka ulendo wokacezela Korneliyo ku Kaisareya.

Korneliyo asonkhanitsa pamodzi apabanja ake ndi anzake apamtima. Pamene Petulo aloŵa, Korneliyo amulandila. Korneliyo agwada pansi ndi kuŵelama pamapazi a Petulo, monga mmene uonela pacithunzi-thunzi apa. Koma Petulo akuti: ‘Imilila, inenso ndine munthu cabe.’ Ndithudi, Baibo imaonetsa kuti n’kulakwa kugwadila munthu kuti umulambile. Tiyenela kulambila Yehova yekha cabe.

Ndiyeno Petulo ayamba kulalikila anthu onse amene asonkhana. Iye akuti: ‘Ndadziŵa tsopano kuti Mulungu amalandila anthu onse amene afuna kumutumikila.’ Ndipo pamene akali kukamba, Mulungu atumiza mzimu wake woyela. Pamenepo anthu ayamba kukamba zinenelo zosiyana-siyana. Zimenezi zidabwitsa kwambili ophunzila aciyuda amene anabwela ndi Petulo, cifukwa io anali kuganiza kuti Mulungu amalandila Ayuda cabe. Conco zimenezi ziwaphunzitsa kuti Mulungu samaona anthu a mtundu umodzi kukhala abwino kapena ofunika kwambili kupambana mitundu ina. Imeneyi ni nkhani yofunika kwambili kwa ife tonse kuikumbukila!

Machitidwe 10:1-48; 11:1-18; Chivumbulutso 19:10.