Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 110

Timoteyo—Mthandizi Watsopano Wa Paulo

Timoteyo—Mthandizi Watsopano Wa Paulo

MWAMUNA wacinyamata amene uona pacithunzi-thunzi apa, amene ali ndi mtumwi Paulo ni Timoteyo. Iye amakhala ku Lustra ndi apabanja lake. Dzina la amai ake ni a Yunike ndipo la ambuye ake ni a Loisi.

Iyi ni nthawi yacitatu imene Paulo acezela Lustra. Papita pafupi-fupi caka cimodzi kucokela pamene Paulo ndi Barnaba anabwela nthawi yoyamba mumzinda umenewu paulendo wao wolalikila. Koma paulendowu Paulo wabwelanso ndi mnzake wina, Sila.

Kodi udziŵa zimene Paulo auza Timoteyo? Iye amufunsa kuti: ‘Kodi ufuna kuti ine ndi Sila tiyendele nawe pamodzi? Ungatithandize kulalikila anthu a m’madela akutali.’

Timoteyo ayankha kuti: ‘Inde, nifuna kuyenda nanu.’ Conco sipanapite nthawi, Timoteyo asiya abanja lake ndipo ayenda pamodzi ndi Paulo ndi Sila. Koma tikalibe kuphunzila za ulendo wao, tiye coyamba tione zimene zimucitikila Paulo. Papita zaka pafupi-fupi 17 kucokela pamene Yesu anaonekela kwa iye paulendo wake wa ku Damasiko.

Kumbukila kuti Paulo anayenda ku Damasiko kuti akazunze ophunzila a Yesu, koma tsopano naye ni wophunzila wa Yesu! Pambuyo pake adani ena afuna kupha Paulo cifukwa io sakondwela ndi zimene iye aphunzitsa ponena za Yesu. Koma ophunzila athandiza Paulo kuthaŵa. Amuika m’basiketi ndi kumutulutsila kunja kwa mpanda wa mzinda.

Pambuyo pake, Paulo apita ku Antiokeya kukalalikila. Otsatila a Yesu ayamba kuchulidwa kuti Akristu ku Antiokeya. Ndiyeno Paulo ndi Barnaba atumizidwa kucoka ku Antiokeya kupita ku maiko akutali kuti akalalikile. Mzinda umodzi umene apitako ni wa Lusitara, kwao kwa Timoteyo.

Tsopano, patapita pafupi-fupi caka cimodzi, Paulo abwelela ku Lustra paulendo wake waciŵili. Pamene Timoteyo, Paulo ndi Sila acoka, kodi udziŵa kumene io apita? Yang’ana pa mapu apa, kuti tiphunzilepo madela ena.

Coyamba, apita kudela lapafupi la Ikoniyo, ndiyeno apita kumzinda waciŵili wa Antiokeya. Pambuyo pake, apita ku Torowa, ndiyeno apita ku Filipi, ku Tesalonika ndi ku Bereya. Kodi mzinda wa Atene wauona pa mapu? Paulo alalikila mumzinda umenewu. Pamene acoka kumeneku, alalikila ku Korinto kwa caka cimodzi ndi hafu. Potsilizila pake, aima pang’ono mumzinda wa Efeso. Ndiyeno abwelela ndi boti ku Kaisareya, ndi kupita ku Antiokeya, ndipo Paulo atsala kumeneku.

Conco, Timoteyo ayenda maulendo atali-atali kukathandiza Paulo kulalikila “uthenga wabwino,” ndi kuyambitsa mipingo yambili yacikristu. Kodi iwe ukakula udzakhala mtumiki wokhulupilika wa Mulungu monga Timoteyo?

Machitidwe 9:19-30; 11:19-26; macaputa 13 mpaka 17; 18:1-22.