Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 113

Paulo Ali Ku Roma

Paulo Ali Ku Roma

ONA Paulo am’manga cheni kumanja, ndipo msilikali waciroma amuyang’anila. Paulo ali mu ndende ku Roma. Ayembekezela kufikila nthawi imene Kaisara, mfumu yaciroma adzakamba zimene ayenela kucita kwa iye. Anthu ni ololedwa kumuona pamene ali mu ndende.

Patapita masiku atatu kucokela pamene Paulo anafika ku Roma, atumiza uthenga wakuti akulu-akulu aciyuda abwele kudzamuona. Cifukwa ca zimenezi, Ayuda ambili a mu Roma abwela. Paulo awalalikila za Yesu ndi za ufumu wa Mulungu. Ena akhulupilila ndipo akhala Akristu, koma ena sakhulupilila.

Paulo alalikilanso kwa asilikali osiyana-siyana omuyang’anila. Kwa zaka ziŵili zimene Paulo akhala kumeneku monga mkaidi, alalikila kwa aliyense pamene wapeza mpata. Zotsatilapo zake n’zakuti, ngakhale anthu a mu nyumba ya Kaisara amvela uthenga wabwino wa Ufumu, ndipo ena a io akhala Akristu.

Kodi mlendo uyu amene alemba pathebulo apa ndani? Kodi ungayese kuchula dzina lake? Ameneyu ni Timoteyo. Nayenso Timoteyo panthawi ina anaponyedwa mu ndende cifukwa colalikila Ufumu, koma anamasulidwa. Ndipo wabwela kuno kudzathandiza Paulo. Kodi udziŵa zimene Timoteyo alemba? Tiye tione.

Kodi wakumbukila mzinda wa Filipi ndi wa Efeso mu nkhani namba 110? Paulo anathandiza kuyambitsa mipingo yacikristu m’mizinda imeneyi. Koma pamene ali m’ndende, Paulo alembela makalata mipingo imeneyi. Makalata amenewa apezeka m’Baibo, ndipo amachedwa Aefeso ndi Afilipi. Paulo tsopano auza Timoteyo zimene afunikila kulemba kwa Akristu anzao ku Filipi.

Afilipi anali okoma mtima kwambili kwa Paulo. Pamene iye anali m’ndende anam’tumizila mphatso, ndiyeno Paulo akuwayamikila cifukwa ca mphatso imeneyi. Epafurodito ndiye amene anabweletsa mphatso imeneyi. Tsopano iye anadwala kwambili kutsala pang’ono kufa. Koma anacila ndipo anali wokonzeka kubwelela kunyumba. Ndi amene adzanyamula kalata yocokela kwa Paulo ndi Timoteyo pamene adzabwelela ku Filipi.

Pamene Paulo anali m’ndende, analembanso makalata ena aŵili amene tili nao m’Baibo. Kalata imodzi analembela Akristu a ku mzinda wa Kolose. Kodi ulidziŵa dzina la kalata imeneyi? Imachedwa Akolose. Kalata ina analembela mnzake wapamtima, Filimoni, amene naye anali kukhala ku Kolose. Kalatayo inali yonena za Onesimo wanchito wa Filimoni.

Onesimo anathaŵa Filimoni ndi kuyenda ku Roma. Pamene anali ku Roma anamvela kuti Paulo ali m’ndende kumeneko. Onesimo anayenda kukacezela Paulo, ndipo nayenso anamulalikila. Sipanapite nthawi Onesimo nayenso anakhala Mkristu. Onesimo anayamba kumva cisoni kuti anathaŵa. Conco kodi udziŵa zimene Paulo analemba m’kalata yopita kwa Filimoni?

Anapempha Filimoni kuti amukhululukile Onesimo. Analemba kuti, ‘Ndamuuza kuti abwelele kwa iwe. Koma tsopano si wanchito wako cabe, iye alinso m’bale wacikristu wocita bwino.’ Pamene Onesimo anabwelela ku Kolose, ananyamula makalata aŵili aja, imodzi yopita kwa Akolose ndipo ina kwa Filimoni. Ndipo Filimoni anakondwela kwambili pamene anamva kuti wanchito wake wakhala Mkristu.

Pamene Paulo analembela Afilipi ndi Filimoni, anawalembela uthenga wabwino kwambili. Iye anauza Afilipi kuti, ‘N’tumiza Timoteyo kwa inu, koma inenso ndidzakucezelani posacedwa.’ Ndipo kwa Filimoni analemba kuti, ‘Ukonzeletu malo anga ogona kumeneko.’

Pamene Paulo anamasulidwa, anacezela abale ndi alongo acikristu m’madela ambili. Koma m’kupita kwa nthawi, Paulo anaponyedwanso m’ndende ku Roma. Koma apa tsopano Paulo anadziŵa kuti adzaphedwa. Conco analembela Timoteyo ndi kumuuza kuti abwele mwamsanga. Iye analemba kuti, ‘Ndakhala wokhulupilika kwa Mulungu, ndipo iye adzandipatsa mphoto.’ Patapita zaka zocepa kucokela pamene Paulo anaphedwa, Yerusalemu anaonongedwanso, koma panthawiyi anaonongedwa ndi Aroma.

Koma m’Baibo muli nkhani zambili. Yehova Mulungu anagwilitsila nchito mtumwi Yohane kulemba mabuku otsilizila a m’Baibo, kuphatikizapo buku la Civumbulutso. Buku la m’Baibo limeneli limafotokoza za mtsogolo. Tiye tsopano tiphunzile zimene zidzacitika mtsogolo.

Machitidwe 28:16-31; Afilipi 1:13; 2:19-30; 4:18-23; Aheberi 13:23; Filimoni 1-25; Akolose 4:7-9; 2 Timoteyo 4:7-9.