Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 115

Paradaiso Watsopano pa Dziko

Paradaiso Watsopano pa Dziko

TAONANI mitengo yaitali, maluwa okongola ndi mapiri atali. Kodi pano si pokongola? Onani m’mene mbawala ikudyera m’manja mwa kamnyamata’ko. Onani mikango ndi akavalo aima uko pa dambo’wo. Kodi mungakonde kukhala m’nyumba yokhala pa malo otere?

Mulungu amafuna kuti mukhale ndi moyo kosatha pa dziko lapansi m’paradaiso. Samafuna kuti ali yense akhale ndi zopweteka ndi zowawa zimene anthu amabvutika nazo lero lino. Iri ndiro lonjezo la Baibulo kwa awo amene adzakhala ndi moyo m’paradaiso watsopano: ‘Mulungu adzakhala nawo. Sipadzakhala’nso imfa kapena kulira kapena chowawa. Zinthu zakale zapita.’

Yesu adzatsimikizira kuona kuti kusintha kodabwitsa’ku kwachitika. Kodi mukudziwa kuti zidzachitika liti? Inde, atachotsera dziko kuipa konse ndi anthu oipa. Pajatu, ali pa dziko lapansi Yesu anachiritsa matenda a mtundu uli wonse a anthu, ndipo iye anaukitsa’nso akufa. Anachita izi kusonyeza zimene adzachita pa dziko lonse akadzakhala Mfumu ya ufumu wa Mulungu.

Ganizirani m’mene kudzakhalira kodabwitsa m’paradaiso watsopano wa pa dziko lonse’yo! Yesu, ndi ena amene iye akuwasankha, adzalamulira ali kumwamba. Olamulira’wo adzasamalira ali yense pa dziko lapansi ndi kuona kuti iwo ali okondwa. Tiyeni tione chimene tifunikira kuchita kuti titsimikizire kuti Mulungu adzatipatsa moyo wosatha m’paradaiso wake watsopano.