Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 115

Paladaiso Yatsopano Padziko Lapansi

Paladaiso Yatsopano Padziko Lapansi

ONA mitengo itali-itali, maluŵa okongola ndi mapili atali-atali pacithunzi-thunzi apa. Malo awa ni abwino, si conco? Ona mmene ka insa kadyela padzanja la kamnyamata aka. Ndipo ona mikango ndi mahosi amene aimilila apo m’dambo. Kodi sungakonde kukhala pa nyumba imene ili m’malo ngati amenewa?

Mulungu afuna kuti ukakhale ndi moyo wamuyaya m’paladaiso padziko lapansi. Ndipo safuna kuti uzimvela zoŵaŵa zimene anthu amavutika nazo masiku ano. Lonjezo la m’Baibo kwa anthu amene adzakhala m’paladaiso yatsopano n’lakuti: ‘Mulungu adzakhala nao. Sikudzakhala imfa kapena kulila kapena zopweteka. Zinthu zakale zapita.’

Yesu adzatsimikizila kuti kusintha kwabwino kumeneku kwacitika. Kodi adzacita zimenezi liti? Adzacita zimenezi pambuyo pakuti wayeletsa dziko lapansi mwa kucotsapo voipa ndi anthu onse oipa. Kumbukila kuti pamene Yesu anali padziko lapansi anacilitsa anthu amene anali ndi matenda osiyana-siyana, ndipo anaukitsanso ngakhale akufa. Yesu anacita izi kuonetsa zimene adzacita pamene adzakhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu.

Ganiza cabe mmene mudzakhalila mwabwino m’paladaiso yatsopano padziko lapansi! Yesu, pamodzi ndi anthu amene adzasankha, adzalamulila kucokela kumwamba. Mafumu amenewa adzasamalila aliyense padziko lapansi ndi kutsimikiza kuti munthu aliyense ni wokondwela. Tiye tione zimene tiyenela kucita kuti tikhale otsimikiza kuti Mulungu adzatipatsa moyo wamuyaya m’paladaiso yake yatsopano.

Chivumbulutso 21:3, 4; 5:9, 10; 14:1-3.