Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI 116

M’mene Tingakhalire Kosatha

M’mene Tingakhalire Kosatha

KODI munganene chimene buthu’lo ndi mabwenzi ake akuwerenga? Inde, ndi bukhu lomwe mukuwerenga’li—Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Ndipo akuwerenga nkhani yomwe mukuwerenga’yi—“M’mene Tingakhalire Kosatha.”

Kodi mukudziwa zimene iwo akuphunzira? Choyamba, kuti tifunikira kudziwa Yehova ndi Mwanake Yesu ngati titi tikhale ndi moyo kosatha. Baibulo limati: ‘Iyi ndiyo njira yokhalira kosatha. Kuphunzira za Mulungu mmodzi yekha woona, ndi Mwana amene iye anam’tuma pa dziko pano, Yesu Kristu.’

Kodi tingaphunzire motani za Yehova ndi Mwanake Yesu? Njira imodzi ndiyo mwa kuwerenga Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo poyambira mpaka pa mapeto. Limasimba zochuluka ponena za Yehova ndi Yesu, eti? Limanena’nso zochuluka ponena za zinthu zimene iwo achita ndi zimene adzachita. Koma tifunikira kuchita zina’nso osangowerenga kokha.

Kodi mukuona bukhu liri apo’lo? Ndiro Baibulo. Pemphani wina kukuwerengerani mbali za Baibulo zimene pazikidwa nkhani za bukhu’li. Iro limatipatsa chidziwitso chonse chimene tikufunikira kuti titumikire Yehova moyenera ndi kupeza moyo wosatha. Chotero tipangetu kukhala chizolowezi kuwerenga Baibulo nthawi zonse.

Koma kungophunzira za Yehova ndi Yesu n’kosakwanira. Tingadziwe zochuluka kwambiri za iwo ndi ziphunzitso zao, ndipo komabe n’kusapeza moyo wosatha. Kodi mukudziwa china’nso chofunika?

Tifunikira’nso kukhala ndi moyo mogwirizana ndi zophunziridwa’zo. Kodi mukukumbukira Yudasi Isikariote? Anali mmodzi wa 12 osankhidwa ndi Yesu kukhala atumwi ake. Iye anali ndi chidziwitso chochuluka cha Yehova ndi Yesu. Koma kodi chinam’chitikira n’chiani? Patapita kanthawi anakhala wadyera, napereka Yesu kwa adani ake mosinthana ndi ndalama za siliva 30. Choncho iye sadzalandira moyo wosatha.

Kodi mukukumbukira Gehazi, uja tinam’phunzira m’Nkhani 69? Anafuna zobvala ndi ndalama zimene sizinali zake. Chotero ananama kuti azipeze. Koma Yehova anam’langa. Ife’nso adzitilanga ngati sitimvera malamulo ake.

Koma pali ena ambiri abwino amene anatumikira Yehova nthawi zonse mokhulupirika. Tikufuna kufanana nawo, eti? Mwana’yo Samueli ndiye chitsanzo chabwino chochitsatira. Pajatu, monga momwe tinaonera m’Nkhani 55, iye anali ndi zaka 4 kapena 5 poyamba kutumikira pa chihema. Chotero mosasamala kanthu za kuchepa kwanu, simuli wamng’ono kwakuti sumungatumikire Yehova.

Munthu amene tikufuna’di kum’tsatira ndiye Yesu. Akali kamnyamata, monga momwe tikuonera m’Nkhani 87, anali pa kachisi akulankhula za Atate wake wakumwamba. Tiyeni titsatire chitsanzo chake. Tiyeni tiuze ochuluka monga momwe tingathere za Mulungu wathu wodabwitsa Yehova ndi Mwanake, Yesu. Tikachita izi, tidzakhoza kukhala ndi moyo kosatha m’paradaiso watsopano wa Mulungu pa dziko lapansi.