Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhani 116

Mmene Tingapezele Moyo Wamuyaya

Mmene Tingapezele Moyo Wamuyaya

KODI udziŵa zimene kamtsikana aka ndi anzake aŵelenga? Aŵelenga buku lino limene iwenso uŵelenga—Buku Langa la Nkhani za mu Baibo. Ndipo naonso aŵelenga phunzilo limene iwe uŵelenga, lakuti: “Mmene Tingapezele Moyo Wamuyaya.”

Kodi udziŵa zimene io aphunzila? Coyamba, aphunzila kuti tiyenela kudziŵa Yehova ndi Mwana wake Yesu kuti tikakhale ndi moyo wamuyaya. Baibo imakamba kuti: ‘Njila ya ku moyo wamuyaya ndi iyi. Kuphunzila za Mulungu woona, ndi Mwana wake amene anatuma padziko lapansi, Yesu Kristu.’

Kodi tingaphunzile bwanji za Yehova Mulungu ndi Mwana wake Yesu? Njila imodzi ni kuŵelenga Buku Langa la Nkhani za mu Baibo kucokela kuciyambi mpaka kotsilizila. Buku limeneli limatiuza zambili za Yehova ndi Yesu, si conco? Ndipo limatiuza zinthu zambili zimene io acita ndi zimene adzacita mtsogolo. Koma tiyenela kucita zambili kuposa kuŵelenga cabe buku lino.

Nanga waliona buku lina limene lili pansi apa? Buku limeneli ni Baibo. Kodi pali anakuŵelengelako Baibo, mmene nkhani za mu buku lino zimacokela? Baibo imapeleka mfundo zokwana zimene tonse timafunikila kuti titumikile Yehova m’njila yoyenela, ndi kuti tikapeze moyo wamuyaya. Conco, tifunikila kukhala ndi cizoloŵezi cophunzila Baibo nthawi zonse.

Koma kungophunzila cabe za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu si kokwanila. Tingakhale ndi cidziŵitso cambili ca Yehova ndi Yesu ndi ziphunzitso zao, koma osapeza moyo wamuyaya. Kodi ucidziŵa cina cofunika?

Tifunikilanso kucita zimene timaphunzila. Kodi umukumbukila Yudasi Isikariyoti? Anali mmodzi wa anthu 12 amene Yesu anasankha kukhala atumwi ake. Yudasi anali ndi cidziŵitso kwambili ca Yehova ndi Yesu. Koma n’ciani cinamucitikila? M’kupita kwa nthawi, anayamba kudzikonda, ndipo anapeleka Yesu kwa adani ake pa ndalama 30 za siliva. Conco Yudasi sadzalandilako moyo wamuyaya.

Kodi umukumbukila Gehazi, mwamuna uja amene tinaphunzila m’nkhani namba 69? Iye anali kufuna zovala ndi ndalama zimene sizinali zake. Conco anakamba bodza kuti apatsidwe zinthu zimenezo. Koma Yehova anamulanga. Ndipo naife adzatilanga ngati sitimvela malamulo ake.

Koma pali anthu abwino ambili amene atumikila Yehova mokhulupilika nthawi zonse. Tifunika kukhala monga io, si conco? Samueli wacicepele ni citsanzo cabwino cakuti titsatile. Kumbukila zimene tinaphunzila m’nkhani namba 55, kuti iye anali ndi zaka 4 kapena 5 cabe pamene anayamba kutumikila Yehova pacihema. Conco ngakhale kuti uli ndi zaka zocepa, sindiwe wamng’ono kutumikila Yehova.

Inde, Yesu Kristu ndiye munthu amene tonse tifunika kutsatila. Ngakhale pamene anali kamnyamata monga mmene tionela mu nkhani namba 87, anali pakacisi akukambitsilana ndi anthu za Atate wake wakumwamba. Tiyenela kutsatila citsanzo cake. Tiyenela kuuza anthu ambili za Yehova, Mulungu wathu wabwino ndi mwana wake, Yesu Kristu. Ngati ticita zimenezi, ndiye kuti tidzakhala ndi moyo wamuyaya mu paladaiso yatsopano ya Mulungu padziko lapansi.

Yohane 17:3; Salimo 145:1-21.