Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chiyembekezo Chotsimikizirika cha Akufa

Chiyembekezo Chotsimikizirika cha Akufa

MKAZI wina wa zaka 25 analemba kuti: “Mu 1981 amayi anga olera anamwalira ndi kansa. Imfa yawo inali yovutitsa mtima kwambiri kwa ine ndi mbale wanga woleredwa. Ndinali wazaka 17, ndipo mbale wangayo anali ndi zaka 11. Ndinawalakalaka kwambiri iwo. Popeza ndinaphunzitsidwa kuti iwo anali kumwamba, ndinafuna kudzipha kuti ndikakhale nawo. Iwo anali bwenzi langa lapamtima.”

Kuli koipa kwambiri kuti imfa ili ndi mphamvu ya kutenga munthu amene mumakonda. Ndipo pamene zichitika, lingaliro la kusakhozanso kulankhula, kuseka, kapena kugwirana ndi wokondedwa wanu lingakhale lovuta kwambiri kulipirira. Kupweteka kumeneko sikumafafanizika kwenikweni mwa kuuzidwa kuti wokondedwa wanu ali kumwamba.

Komabe, Baibulo limapereka chiyembekezo chosiyana kwambiri. Monga momwe taonera poyamba, Malemba amasonyeza kuti kuli kotheka kugwirizananso ndi wakufa wanu wokondedwayo mtsogolo posachedwapa, osati kumalo akumwamba osadziŵika koma pompano padziko lapansi m’mikhalidwe yolungama, yamtendere. Ndipo panthaŵiyo anthu adzakhala ndi chiyembekezo chakukhala ndi thanzi langwiro, ndipo sadzamwaliranso. ‘Koma limenelo liyenera kukhala lingaliro chabe lokhumbika!’ ena angatero.

Kodi nchiyani chimene chingakukhutiritseni kuti chiyembekezo chimenechi nchoona? Kuti mukhulupirire lonjezolo, mufunikira kukhala wotsimikizira kuti wopereka lonjezo ali wofunitsitsa ndi wokhoza kulikwaniritsa. Pamenepo, kodi ndani amene akulonjeza kuti akufa adzakhalanso ndi moyo?

M’ngululu ya 31 C.E., Yesu Kristu analengeza molimba mtima kuti: “Monga Atate aukitsa akufa, nawapatsa moyo, momwemonso Mwana apatsa moyo iwo amene Iye afuna. Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda [achikumbukiro, NW] adzamva mawu ake [a Yesu], nadzatulukira.” (Yohane 5:21, 28, 29) Inde, Yesu Kristu analonjeza kuti mamiliyoni amene ali akufa tsopano adzakhalanso ndi moyo padziko lino lapansi ndi kukhala ndi chiyembekezo cha kukhalapobe kwa muyaya m’mikhalidwe yauparadaiso, yamtendere. (Luka 23:43; Yohane 3:16; 17:3; yerekezerani ndi Salmo 37:29 ndi Mateyu 5:5.) Popeza kuti Yesu anapanga lonjezolo, kuli kwanzeru kulingalira kuti iye ali wofunitsitsa kulikwaniritsa. Koma kodi iye ali wokhoza kutero?

Zaka ziŵiri zisanakwane pambuyo popereka lonjezo limenelo, Yesu anasonyeza mwa njira yamphamvu kuti iye ali wofunitsitsa ndi wokhoza kuukitsa.

“Lazaro, Tuluka”!

Chinali chochitika chokhudza mtima. Lazaro anali wodwala kwakayakaya. Alongo ake aŵiri, Mariya ndi Marita, adatumiza mawu kwa Yesu, yemwe anali kutsidya lina la mtsinje wa Yordano kuti: “Ambuye, onani, amene mumkonda adwala.” (Yohane 11:3) Iwo anadziŵa kuti Yesu anakonda Lazaro. Kodi Yesu sakanafuna kuona bwenzi lake lodwalalo? Modabwitsa, mmalo mopita ku Betaniya mwamsanga, Yesu anakhalabe kumene anali kwa masiku ena aŵiri.​—Yohane 11:5, 6.

Lazaro anamwalira pambuyo pakuti uthenga wa kudwala kwake watumizidwa kale. Yesu anadziŵa pamene Lazaro anamwalira, ndipo anafuna kuchitapo kanthu. Pofika nthaŵi imene Yesu anafika mu Betaniya, bwenzi lake lokondedwalo linali lakufa kwa masiku anayi. (Yohane 11:17, 39) Kodi Yesu akakhoza kuukitsa munthu amene wakhala wakufa kwa utali wonsewo?

Atamva kuti Yesu akubwera, Marita, mkazi wokangalika, anatuluka kukamchingamira. (Yerekezerani ndi Luka 10:38-42.) Atakhudzidwa ndi chisoni cha mkaziyo, Yesu anamtsimikizira kuti: “Mlongo wako adzauka.” Pamene mkaziyu anasonyeza chikhulupiriro chake cha chiukiriro, Yesu anamuuza poyera kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo.”​—Yohane 11:20-25.

Atafika pamandapo, Yesu anawauza kuti achotse mwala wotseka pakhomo pa mandawo. Ndiyeno, atapemphera mofuula, analamula kuti: “Lazaro, tuluka”!​—Yohane 11:38-43.

Onse anali maso dwii pamandapo. Kenako, mumdimamo munatuluka munthu. Miyendo ndi manja ake anali omanga ndi nsalu zakumanda, ndipo nkhope yake inalinso yokulungidwa ndi nsalu. “Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke,” analamula motero Yesu. Nsalu zomalizira zomasulidwazo zinagwera pansi. Inde, analidi Lazaro, mwamuna yemwe anakhala wakufa kwa masiku anayi!​—Yohane 11:44.

Kodi Zinachitikadi?

Nkhani ya kuukitsidwa kwa Lazaro ikusimbidwa mu Uthenga Wabwino wa Yohane monga chochitika chenicheni cha m’mbiri. Zoloŵetsedwamo nzoonekera bwino kwambiri kwakuti sizingakhale nthano chabe. Kukayikira kuchitika kwake m’mbiri ndiko kukayikira zozizwitsa zonse za m’Baibulo, kuphatikizapo chiukiriro cha Yesu Kristu mwiniyo. Ndipo kukana chiukiriro cha Yesu ndiko kukana chikhulupiriro chonse Chachikristu.​—1 Akorinto 15:13-15.

Kwenikweni, ngati muvomereza kukhalako kwa Mulungu, simuyenera kukhala ndi vuto la kukhulupirira chiukirirocho. Nachi chitsanzo: Munthu akhoza kujambulitsa pa tepu ya vidiyo kuŵerenga kwake chikalata chalamulo chotchula amene ayenera kugaŵiridwa chuma chake pa imfa yake, ndipo atamwalira, achibale ake ndi mabwenzi akhoza kumuona ndi kumumva pamene akulongosola mmene chuma chake chiyenera kugaŵidwira. Zaka zana limodzi kumbuyoku, chinthu choterocho chinali chosalingalirika. Ndipo kwa anthu ena lerolino okhala m’mbali zakutali za dziko lapansi, sayansi ya kujambula ndi vidiyo ili yovuta kumva monga chozizwitsa. Ngati malamulo asayansi oyikidwa ndi Mlengi angagwiritsiridwe ntchito ndi anthu kupanganso chithunzithunzi chooneka ndi chomveka mawu chotero, kodi Mlengiyo sangakhoze kuchita zoposa? Pamenepo, kodi sikuli kwanzeru kuti Iye amene analenga moyo ali wokhoza kuulenganso?

Chozizwitsa cha kubwezeretsa Lazaro ku moyo chinathandiza kukulitsa chikhulupiriro mwa Yesu ndi chiukiriro. (Yohane 11:41, 42; 12:9-11, 17-19) Mwa njira yogwira mtima, chimasonyezanso kufunitsitsa ndi chikhumbo cha Yehova ndi Mwana wake cha kuukitsa anthu.

‘Mulungu Adzakhala ndi Chikhumbo’

Kachitidwe ka Yesu pa imfa ya Lazaro kamasonyeza chifundo cha Mwana wa Mulungu. Chisoni chake chachikulu pa chochitika chimenechi chimasonyeza bwino lomwe chikhumbo chake chachikulu cha kuukitsa akufa. Timaŵerenga kuti: “Pomwepo Mariya, pofika pamene panali Yesu, mmene anamuona Iye, anagwa pa mapazi ake, nanena ndi Iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira. Pamenepo Yesu, pakumuona iye alikulira, ndi Ayuda akumperekeza iye alikulira, anadzuma mumzimu, navutika mwini, nati, Mwamuika iye kuti? Ananena ndi Iye, Ambuye, tiyeni, mukaone. Yesu analira. Chifukwa chake Ayuda ananena, Taonani, anamkondadi!”​—Yohane 11:32-36.

Chifundo cha Yesu chochokera pansi pa mtima chikusonyezedwa panopo ndi mawu atatu akuti: “anadzuma mumzimu,” “navutika mwini,” ndi akuti “analira.” Mawu a chinenero choyambirira ogwiritsiridwa ntchito polemba chochitika chokhudza mtima chimenechi amasonyeza kuti Yesu anachita chisoni kwambiri ndi imfa ya bwenzi lake lapamtima Lazaro ndi poona mlongo wa Lazaro akulira kotero kuti maso Ake anadzaza misozi. *

Chapadera kwambiri nchakuti Yesu anali ataukitsa kale anthu aŵiri. Ndipo anafunitsitsa kuchitanso chimodzimodzi kwa Lazaro. (Yohane 11:11, 23, 25) Komabe, iye “analira.” Chotero, kubwezeretsa anthu ku moyo sikuli chabe mchitidwe wamba kwa Yesu. Chifundo chake ndi chisoni chachikulu zosonyezedwa pachochitikachi zimasonyeza bwino lomwe chikhumbo chake chachikulu cha kubwezeretsa otengedwa ndi imfa.

Chifundo cha Yesu poukitsa Lazaro chinasonyeza chikhumbo chake chachikulu cha kubwezeretsa awo otengedwa ndi imfa

Popeza kuti Yesu ali ‘chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe cha [Yehova Mulungu, NW],’ moyenerera sitingayembekezere zochepa kwa Atate wathu wakumwamba. (Ahebri 1:3) Ponena za chifuno cha Yehova mwiniyo cha kuukitsa anthu, mwamuna wokhulupirika Yobu anati: “Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? . . . Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani; mukadakhumba ntchito ya manja anu.” (Yobu 14:14, 15) Panopo liwu la chinenero choyambirira limene linamasuliridwa kuti “mukadakhumba” limasonyeza kufunitsitsa koona mtima kwa Mulungu ndi chikhumbo chake. (Genesis 31:30; Salmo 84:2) Mwachionekere, Yehova ayenera kukhala akulakalaka kwambiri kufika kwa nthaŵi ya chiukiriro.

Kodi tingakhulupiriredi lonjezo la chiukiriro? Inde, palibe chikayikiro kuti Yehova ndi Mwana wake ali ofunitsitsa ndi okhoza kuchikwaniritsa. Kodi zimenezi zimatanthauzanji kwa inu? Muli ndi chiyembekezo cha kugwirizanitsidwanso ndi okondedwa anu akufawo pompano padziko lapansi koma m’mikhalidwe yosiyana kwambiri!

Yehova Mulungu, amene anayambitsa mtundu wa anthu m’munda wokongola, walonjeza kubwezeretsa Paradaiso pa dziko lapansi pano pansi pa ulamuliro wa Ufumu Wake wakumwamba wokhala m’manja mwa Yesu Kristu yemwe tsopano ali paulemerero. (Genesis 2:7-9; Mateyu 6:10; Luka 23:42, 43) Mu Paradaiso wobwezeretsedwayo, banja la anthu lidzakhala ndi chiyembekezo cha kusangalala ndi moyo kosatha, popanda kudwala nthenda iliyonse. (Chivumbulutso 21:1-4; yerekezerani ndi Yobu 33:25; Yesaya 35:5-7.) Zimene zidzakhalanso zitatha ndizo chidani chonse, tsankho la fuko, chiŵaŵa pa mafuko, ndi vuto la chuma. Lidzakhala dziko lapansi loyeretsedwa mmene Yehova Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu adzaukitsiramo akufa.

Chiukiriro, chozikidwa pa nsembe yadipo ya Kristu Yesu, chidzabweretsa chisangalalo kwa mitundu yonse

Chimenecho tsopano ndicho chiyembekezo cha mkazi Wachikristu yemwe tatchula pachiyambi cha chigawo chino. Zaka zingapo pambuyo pa kumwalira kwa amayi ake, Mboni za Yehova zinamthandiza kuphunzira Baibulo mosamalitsa. Iye akukumbukira kuti: “Nditaphunzira za chiyembekezo cha chiukiriro, ndinalira. Kunali kodabwitsa kudziŵa kuti amayi ndidzawaonanso.”

Ngati nanunso mtima wanu umakhumba kuonanso wokondedwa wanu, Mboni za Yehova zidzakhala zosangalala kukuthandizani kuphunzira mmene mungapezere chiyembekezo chotsimikizirika chimenechi. Bwanji osaonana nazo pa Nyumba Yaufumu yapafupi ndi kwanuko, kapena lemberani ku keyala yapafupi yondandalikidwa patsamba 32.

^ ndime 20 Liwu Lachigiriki lomasuliridwa kuti “anadzuma mumzimu” likuchokera ku mneni wakuti (em·bri·maʹo·mai) amene amatanthauza kukhudzidwa mtima kopweteka, kapena kwakukulu. Katswiri wina wa Baibulo akunena kuti: “Panopa lingangotanthauza kuti chisoni chachikulu chinagwira Yesu kotero kuti kudzuma kunangotuluka kokha mumtima Wake.” Liwu lotembenuzidwa kuti ‘kuvutika mwini’ likuchokera ku liwu Lachigiriki (ta·rasʹso) limene limasonyeza kuvutika mtima. Malinga ndi kunena kwa wolemba dikishonale, limatanthauza “kuchititsa munthu kusautsika mumtima, . . . kukhudzidwa ndi kupwetekedwa kapena chisoni chachikulu.” Liwu lakuti “analira” limachokera ku mneni Wachigiriki (da·kryʹo) amene amatanthauza “kugwetsa misoni, kulira mwakachetechete.”