Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mawu Oyamba

Mawu Oyamba

Wokondedwa Wowerenga Bukuli:

Kodi mumaona kuti ndinu woyandikana ndi Mulungu? Anthu ambiri amaona kuti n’zosatheka. Ena amalingalira kuti iye alibe chidwi ndi anthu, pamene ena amadziona kuti ndi osanunkha kanthu m’pang’ono pomwe moti sangayembekezere kuyandikana naye. Komabe, Baibulo limatilimbikitsa mwachikondi kuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.” (Yakobo 4:8) Mulungu amatsimikizira omulambira ake kuti: “Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usaope ndidzakuthandiza iwe.”​—Yesaya 41:13.

Kodi tingachitenji kuti tikhale ndi unansi wabwino woterewu ndi Mulungu? Pa ubwenzi uliwonse umene timapanga, timagwirizana ndi munthuyo chifukwa chakuti timamudziŵa, ndiponso kuti ali ndi khalidwe lapadera limene timalisirira ndi kuliona kukhala labwino zedi. Motero makhalidwe a Mulungu ndiponso kachitidwe kake ka zinthu, monga zasonyezedwera m’Baibulo, ndi nkhani yofunika kwambiri kuiphunzira. Pamene tisinkhasinkha mmene Yehova amaonetsera mbali iliyonse ya makhalidwe ake, pamene tiona mmene Yesu Kristu anasonyezera bwino kwambiri makhalidwe amenewo, ndiponso pamene timvetsetsa mmene ifenso tingakulitsire makhalidwewo, tidzamuyandikira kwambiri Mulungu. Tidzaona kuti mwalamulo Yehova ndiye Wolamulira Wamkulu ndi woyenerera wa chilengedwe chonse. Ndiponso, ndiye Atate amene tonsefe timafunikira. Pokhala wamphamvu, wachilungamo, wanzeru, ndi wachikondi, sanyanyala ana ake okhulupirika.

Tikukhumba kuti buku lino likuthandizeni kuyandikira kwambiri kwa Yehova Mulungu, ndi kuti mugwirizane naye nthaŵi zonse kuti mukamutamande kosatha.

Ofalitsa