Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 2

Kodi N’zothekadi ‘Kuyandikira Mulungu’?

Kodi N’zothekadi ‘Kuyandikira Mulungu’?

1, 2. (a) N’chiyani chimene anthu ambiri angaone kuti n’chosatheka, koma kodi Baibulo limatitsimikizira chiyani? (b) Kodi Abulahamu anapatsidwa mwayi wotani, ndipo n’chifukwa chiyani?

 KODI mungamve bwanji ngati Mulungu amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi atanena za inuyo kuti, “Uyu ndi mnzanga”? Anthu ambiri angaone kuti zimenezi n’zosatheka. Angamaganize kuti zingatheke bwanji kuti munthu akhale mnzake wa Yehova Mulungu? Komatu Baibulo limatitsimikizira kuti n’zotheka kuyandikira Mulungu.

2 Abulahamu, yemwe anakhalapo kalekale, anali pa ubwenzi woterewu ndi Yehova ndipo iye anamutchula kuti “mnzanga.” (Yesaya 41:8) Yehova ankaona kuti Abulahamu ndi mnzake wapamtima. Abulahamu anali ndi mwayi umenewu chifukwa “anakhulupirira zimene Yehova anamuuza.” (Yakobo 2:23) Masiku anonso, Yehova amafuna kuti anthu amene amamutumikira akhale anzake ‘n’kumawasonyeza chikondi.’ (Deuteronomo 10:15) Baibulo limatiuza kuti: “Yandikirani Mulungu ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yakobo 4:8) Kodi mawu amenewa akutanthauza chiyani?

3. Kodi Yehova akutiuza kuti tichite chiyani, ndipo akulonjeza kuti adzachita chiyani?

3 Yehova akutiuza kuti timuyandikire. Iye ndi wokonzeka ndiponso wofunitsitsa kuti tikhale anzake. Komanso akulonjeza kuti tikamuyandikira, iyenso adzatiyandikira. Choncho tingakhale “pa ubwenzi wolimba” ndi Yehova, womwe ndi mwayi wamtengo wapatali. (Salimo 25:14) Munthu amene uli naye “pa ubwenzi wolimba” ndi mnzako amene umatha kumuuza zinthu zachinsinsi zomwe sungauze aliyense.

4. Kodi mnzathu wapamtima amachita zotani, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ali ngati mnzathu ameneyo?

4 Kodi muli ndi mnzanu wapamtima amene mumamuuza zakukhosi? Mnzanu wotereyu amakukondani kwambiri komanso mumamudalira chifukwa amasonyeza kuti ndi wokhulupirika. Mumasangalala kwambiri mukamakambirana zinthu zimene zimakusangalatsani. Mukamamufotokozera mavuto anu, amasonyeza kuti akukuderani nkhawa ndipo zimenezi zimachititsa kuti mumveko bwino. Iye amakumvetsani ngakhale pamene zikuoneka kuti palibe yemwe akukumvetsani. Mofanana ndi zimenezi, mukayandikira Mulungu, mumakhala ndi Mnzanu wapadera amene amaona kuti ndinu wofunika, amakuganizirani ndiponso amakumvetsetsani kuposa aliyense. (Salimo 103:14; 1 Petulo 5:7) Mumakhulupirira kuti mungathe kumuuza chilichonse chifukwa mumadziwa kuti ndi wokhulupirika kwa anthu omwenso ndi okhulupirika kwa iye. (Salimo 18:25) Komabe, mwayi wokhala anzake a Mulungu umatheka chifukwa cha zimene iye anachita.

Yehova Anatsegula Njira

5. Kodi Yehova anachita chiyani kuti tithe kukhala naye pa ubwenzi?

5 Popeza ndife ochimwa, patokha sitikanatha kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. (Salimo 5:4) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Koma Mulungu akutisonyeza chikondi chake, chifukwa pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.” (Aroma 5:8) Yehova anakonza kuti Yesu ‘adzapereke moyo wake dipo kuti awombole anthu ambiri.’ (Mateyu 20:28) Tikamakhulupirira nsembe ya dipo imeneyi, timatha kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. Popeza Mulungu ndi amene ‘anayamba kutikonda,’ anakonza zoti tikhale naye pa ubwenzi.​—1 Yohane 4:19.

6, 7. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova si Mulungu wobisika yemwe sitingathe kumudziwa? (b) Kodi Yehova wagwiritsa ntchito njira ziti kuti timudziwe?

6 Palinso zinthu zina zimene Yehova wachita. Iye watidziwitsa zokhudza iyeyo. Kuti munthu akhale mnzathu wapamtima timafunika kumudziwa bwino. Timafunika kudziwa makhalidwe ake komanso mmene amachitira zinthu. Choncho Yehova akanakhala kuti ndi Mulungu wobisika ndiponso wosatheka kumudziwa, sizikanatheka kuti akhale mnzathu. Komatu Yehova sadzibisa ndipo amafuna kuti timudziwe. (Yesaya 45:19) Komanso iye amalola kuti aliyense amudziwe, ngakhalenso anthu amene dzikoli limawaona kuti ndi otsika moti sangathe kudziwa Mulungu.​—Mateyu 11:25.

Yehova watithandiza kuti timudziwe pogwiritsa ntchito zimene analenga komanso Baibulo

7 Kodi Yehova wagwiritsa ntchito chiyani kuti timudziwe? Zinthu zimene analenga zimatithandiza kudziwa makhalidwe ake ena monga mphamvu zake zopanda malire, nzeru zake zakuya komanso chikondi chake chachikulu. (Aroma 1:20) Koma pali njira inanso imene Yehova wagwiritsa ntchito kuti timudziwe. Iye amatiuza zambiri kudzera m’Mawu ake, Baibulo.

Yehova Amatiuza Zokhudza Iyeyo Kudzera M’Baibulo

8. Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti Baibulo palokha ndi umboni wakuti Yehova amatikonda?

8 Mmene Baibulo linalembedwera ndi umboni wakuti Yehova amatikonda. Amadzifotokoza m’njira yosavuta ndipo zimenezi zimasonyeza kuti amafuna kuti timudziwe ndiponso tizimukonda. Zimene timawerenga m’buku lamtengo wapatali limeneli, zimatithandiza kuti Yehova akhale mnzathu. (Salimo 1:1-3) Tiyeni tikambirane njira zina zosangalatsa zimene Yehova anagwiritsa ntchito m’Mawu ake potithandiza kuti timudziwe.

9. Kodi ndi malemba ati amene amatchula mosapita m’mbali makhalidwe a Mulungu?

9 M’Baibulo muli mawu ambiri amene amatchula mosapita m’mbali makhalidwe a Mulungu. Taonani zitsanzo izi. “Yehova amakonda chilungamo.” (Salimo 37:28) Mulungu “ali ndi mphamvu zazikulu.” (Yobu 37:23) “‘Ndine wokhulupirika,’ akutero Yehova.” (Yeremiya 3:12) “Iye ali ndi mtima wanzeru.” (Yobu 9:4) Iye ndi “Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga ndiponso wachikondi chokhulupirika chochuluka komanso choonadi.” (Ekisodo 34:6) “Inu Yehova ndinu wabwino ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.” (Salimo 86:5) Ndipo mogwirizana ndi zimene tanena m’mutu wapitawu, ali ndi khalidwe lina lomwe limaposa makhalidwe ena onse. Baibulo limati: “Mulungu ndi chikondi.” (1 Yohane 4:8) Tikamaganizira kwambiri za makhalidwe osangalatsa amenewa, timafunitsitsa kuti Mulungu akhale mnzathu.

10, 11. (a) Kodi Yehova anaikanso chiyani m’Baibulo pofuna kutithandiza kudziwa bwino makhalidwe ake? (b) Kodi ndi chitsanzo chiti cha m’Baibulo chimene chimatithandiza kuona mmene Mulungu amagwiritsira ntchito mphamvu zake?

10 Kuwonjezera pa kutiuza makhalidwe ake m’Baibulo, mwachikondi Yehova anaikamonso zitsanzo za mmene anasonyezera makhalidwewo pochita zinthu ndi anthu. Tikamawerenga nkhani zimenezi, timakhala ngati tikuona zinthuzo m’maganizo mwathu ndipo zimatithandiza kumudziwa bwino Yehova komanso kukhala naye pa ubwenzi. Taonani chitsanzo ichi.

Baibulo limatithandiza kuyandikira kwa Yehova

11 Munthu sangadziwe zambiri ngati atangowerenga kuti Mulungu “ali ndi mphamvu zambiri zochitira zinthu.” (Yesaya 40:26) Koma akhoza kumvetsa mfundoyi ngati atawerenga za mmene Mulungu analanditsira Aisiraeli pa Nyanja Yofiira kenako n’kumawasamalira m’chipululu kwa zaka 40. Yerekezerani kuti mukuona madzi oyenda mwamphamvu akugawanika. Kenako mukuona Aisiraeli, mwina anthu okwana 3 miliyoni, akuyenda panyanjapo panthaka youma, madzi ataundana n’kukhala ngati makoma akuluakulu kumbali zonse ziwiri. (Ekisodo 14:21; 15:8) Mungaonenso umboni wakuti Yehova ankawateteza komanso kuwasamalira bwino m’chipululu. Anawapatsa madzi kuchokera m’thanthwe. Ankawapatsa chakudya chooneka ngati njere zoyera chomwe chinkagwa kuchokera kumwamba. (Ekisodo 16:31; Numeri 20:11) Zimenezi zikusonyeza kuti sikuti Yehova ali ndi mphamvu zokha, koma kuti amagwiritsanso ntchito mphamvuzo pothandiza anthu ake. Kodi si zolimbikitsa kudziwa kuti mapemphero athu amapita kwa Mulungu wamphamvu amene “ndi pothawira pathu komanso mphamvu yathu, thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya mavuto”?​—Salimo 46:1.

12. Kodi Yehova amatithandiza bwanji kuti timudziwe pogwiritsa ntchito mawu omwe tingawamvetse?

12 Yehova, yemwe ndi Mzimu, wachitanso zina zambiri potithandiza kuti timudziwe. Anthufe timangoona zinthu zooneka, choncho sitingathe kuona zomwe zili kumwamba komwe Yehova amakhala. Ngati Mulungu akanatiuza zokhudza iyeyo pogwiritsa ntchito mawu amene anthu sangawadziwe, zikanakhala zofanana ndi kuuza munthu yemwe anabadwa wosaona mmene maso anu kapena khungu lanu limaonekera. Komabe Yehova mokoma mtima amagwiritsa ntchito mawu omwe tingawamvetse potithandiza kuti timudziwe. Nthawi zina amadziyerekezera ndi zinthu zimene timazidziwa. Penanso amadzifotokoza ngati kuti ali ndi ziwalo zina za munthu. a

13. Kodi lemba la Yesaya 40:11 limatipangitsa kuti tiziganizira zotani, nanga zimenezo zimakukhudzani bwanji?

13 Taonani zimene lemba la Yesaya 40:11 likunena zokhudza Yehova: “Iye adzasamalira gulu la nkhosa zake ngati m’busa. Ndi dzanja lake, adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa, ndipo adzawanyamulira pachifuwa pake.” Palembali Yehova akumuyerekeza ndi m’busa amene amanyamula ana a nkhosa ndi “dzanja lake.” Izi zikusonyeza kuti Mulungu ali ndi mphamvu zotha kuteteza ndiponso kuthandiza anthu ake, ngakhale amene amaoneka kuti ndi osowa thandizo. Tingakhale otetezeka m’manja ake amphamvu, chifukwa ngati tili okhulupirika, iye sadzatisiya. (Aroma 8:38, 39) Yehova, M’busa Wamkulu, amanyamula ana a nkhosa “pachifuwa pake.” Mawuwa amanena za chovala chakumtunda chomwe nthawi zina m’busa ankachipinda n’kunyamulirapo mwana wa nkhosa wobadwa kumene. Choncho zimenezi zikutitsimikizira kuti Yehova amaona kuti ndife amtengo wapatali ndiponso amatisamalira mwachikondi. Izi zimachititsa kuti tizifuna kuti akhale mnzathu.

‘Mwana Amafuna Kuulula za Atate’

14. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova amatithandiza kuti timudziwe bwino pogwiritsa ntchito Yesu?

14 M’Mawu ake, Yehova amathandiza anthu kuti amudziwe pogwiritsa ntchito Mwana wake wokondedwa, Yesu. Palibe amene akanasonyeza bwino maganizo a Mulungu komanso mmene amamvera, kapenanso yemwe akanamufotokoza bwino kuposa mmene Yesu anachitira. Ndipotu Mwana woyamba kubadwayu anali ndi Atate wake, angelo komanso chilichonse chisanalengedwe. (Akolose 1:15) Yesu ankamudziwa bwino kwambiri Yehova. N’chifukwa chake ananena kuti: “Palibe amene akumudziwa bwino Mwana koma Atate okha. Komanso palibe amene akuwadziwa bwino Atate koma Mwana yekha ndi aliyense amene Mwanayo wafuna kumuululira za Atatewo.” (Luka 10:22) Ali padziko lapansi, Yesu anathandiza anthu kudziwa Atate wake m’njira ziwiri zofunika kwambiri.

15, 16. Kodi Yesu anathandiza anthu kudziwa Atate ake m’njira ziwiri ziti?

15 Njira yoyamba ndi zimene Yesu anaphunzitsa. Yesu anafotokoza zokhudza Yehova mogwira mtima. Mwachitsanzo, pofotokoza kuti Mulungu ndi wachifundo ndipo amalandiranso ochimwa amene alapa, Yesu anayerekeza Yehova ndi bambo wokhululuka yemwe anasonyeza chifundo ataona mwana wake wolowerera akubwerera kunyumba. Bamboyo anathamangira mwanayo n’kumuhaga komanso kumukisa. (Luka 15:11-24) Yesu anaphunzitsanso kuti Yehova ‘amakoka’ anthu a mitima yabwino chifukwa amawakonda aliyense payekha. (Yohane 6:44) Ngakhalenso mpheta ikagwa pansi, Yehova amadziwa. Yesu anati: “Musachite mantha, ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zambiri.” (Mateyu 10:29, 31) Apatu sitingachitirenso mwina koma kuyesetsa kuti Mulungu wachikondiyu akhale mnzathu.

16 Njira yachiwiri ndi chitsanzo cha Yesu. Iye anasonyeza bwino kwambiri mmene Atate ake alili moti ananena kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yohane 14:9) Choncho, tikamawerenga m’mabuku a Uthenga Wabwino zokhudza mmene Yesu ankamvera komanso mmene ankachitira zinthu ndi anthu, zimakhala ngati tikuona Atate ake. Palibenso njira ina imene Yehova akanagwiritsa ntchito potithandiza kudziwa makhalidwe ake kuposa imeneyi. N’chifukwa chiyani tikutero?

17. Perekani chitsanzo cha zimene Yehova wachita potithandiza kumvetsa kuti iye ndi wotani.

17 Taganizirani chitsanzo ichi: Tiyerekeze kuti munthu wina wakufunsani kuti kukoma mtima kumatanthauza chiyani. Mwina mukhoza kumufotokozera tanthauzo lake. Koma ngati mungaloze munthu yemwe wachita zinthu mokoma mtima n’kunena kuti, “Zimene wachitazi ndiye kukoma mtima,” munthu angamvetse bwino tanthauzo la mawuwa. Yehova wachita zofanana ndi zimenezi potithandiza kuti timvetse zokhudza iyeyo. Kuwonjezera pa kutifotokozera kuti iye ndi wotani, watipatsanso chitsanzo chabwino cha Mwana wake. Zimene Yesu ankachita ali padziko lapansi, zimatithandiza kumvetsa makhalidwe a Mulungu. Tikamawerenga zokhudza Yesu m’mabuku a Uthenga Wabwino, zimakhala ngati Yehova akutiuza kuti: “Ndi mmenenso ine ndilili.” Ndiye kodi nkhani zouziridwazi zimafotokoza zotani zokhudza Yesu?

18. Kodi Yesu anasonyeza bwanji mphamvu, chilungamo ndiponso nzeru?

18 Yesu anasonyeza bwino kwambiri makhalidwe 4 akuluakulu a Mulungu. Iye anali ndi mphamvu ndipo ankatha kuchiritsa odwala, kudyetsa anjala ngakhalenso kuukitsa akufa. Koma mosiyana ndi anthu odzikonda amene amagwiritsa ntchito molakwika mphamvu zawo, iye sanagwiritse ntchito mphamvu pochita zodabwitsa kuti adzipindulitse kapenanso kuti avulaze ena. (Mateyu 4:2-4) Yesu ankakonda chilungamo. Iye anakwiya kwambiri ataona amalonda achinyengo akubera anthu. (Mateyu 21:12, 13) Analibe tsankho ndipo anthu osauka komanso oponderezedwa sankawasala koma ankawathandiza kuti ‘atsitsimulidwe.’ (Mateyu 11:4, 5, 28-30) Zimene ankaphunzitsa zinkasonyeza kuti anali ndi nzeru kuposa aliyense ngakhalenso Solomo. (Mateyu 12:42) Koma Yesu sankachita zinthu modzionetsera kuti ndi wanzeru. Mawu ake ankawafika pamtima anthu wamba chifukwa zimene ankaphunzitsa zinali zomveka bwino, zosavuta ndiponso zothandiza.

19, 20. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yosonyeza chikondi? (b) Kodi tizikumbukira chiyani tikamawerenga komanso kuganizira chitsanzo cha Yesu?

19 Yesu anali chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yosonyeza chikondi. Pa nthawi yonse ya utumiki wake, iye anasonyeza chikondi m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, akaona anthu akuvutika ankamva chisoni. Ndipo nthawi zonse mtima wachisoni umenewu unkamuchititsa kuti awathandize. (Mateyu 14:14) Ngakhale kuti ankachiritsa odwala ndiponso kudyetsa anjala, Yesu anasonyezanso chifundo m’njira ina yofunika kwambiri. Anathandiza anthu kuti adziwe choonadi cha Ufumu wa Mulungu, womwe udzathandize anthu kuti asamavutikenso. Anawathandizanso kuti azikonda kwambiri choonadicho. (Maliko 6:34; Luka 4:43) Koposa zonse, Yesu anasonyeza chikondi chololera kuvutikira ena popereka moyo wake mofunitsitsa kuti apulumutse anthu.​—Yohane 15:13.

20 Ndiye kodi n’zodabwitsa kuti anthu a misinkhu yonse ndiponso azikhalidwe zosiyanasiyana ankakopeka ndi munthu wachikondi ameneyu? (Maliko 10:13-16) Komabe nthawi zonse tikamawerenga ndiponso kuganizira zimene Yesu anachita, tizikumbukira kuti kudzera mwa Mwana ameneyu timatha kudziwa bwino zokhudza Atate ake.​—Aheberi 1:3.

Bukuli Likuthandizani Kuphunzira za Yehova

21, 22. Kodi tingafunefune bwanji Yehova, nanga m’bukuli muli zinthu ziti zomwe zingatithandize kuchita zimenezi?

21 Popeza Yehova watithandiza kumudziwa bwino kudzera m’Baibulo, n’zodziwikiratu kuti amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi. Koma sikuti iye amatikakamiza kuti tichite zimenezi. Zili ndi ife kumufunafuna pamene “adakali pafupi.” (Yesaya 55:6) Timafunafuna Yehova tikamayesetsa kudziwa makhalidwe ake ndiponso mmene amachitira zinthu mogwirizana ndi zimene zafotokozedwa m’Baibulo. Buku limene mukuwerengali lakonzedwa kuti likuthandizeni kuchita zimenezi.

22 Muona kuti bukuli lagawidwa m’zigawo 4 mogwirizana ndi makhalidwe akuluakulu 4 a Yehova omwe ndi mphamvu, chilungamo, nzeru ndi chikondi. Chigawo chilichonse chikuyamba n’kufotokoza khalidwelo mwachidule. Mitu yotsatira m’chigawocho ikufotokoza mmene Yehova amasonyezera khalidwelo m’njira zosiyanasiyana. M’chigawo chilichonse mulinso mutu umene ukufotokoza mmene Yesu anasonyezera khalidwelo, komanso mutu wina womwe ukufotokoza mmene ifeyo tingalisonyezere pa moyo wathu.

23, 24. (a) Fotokozani cholinga cha bokosi lakuti “Mafunso Ofunika Kuwaganizira.” (b) Kodi kuganizira mozama kumatithandiza bwanji kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Mulungu?

23 Kuyambira mutu uno, pali bokosi lapadera lakuti “Mafunso Ofunika Kuwaganizira.” Mwachitsanzo, taonani  bokosili patsamba 24. Malemba komanso mafunsowo sanakonzedwe n’cholinga choti mubwereze zimene zili m’mutuwo. Cholinga chake n’kukuthandizani kuganizira mbali zina zofunika za nkhani imene tafotokozayo. Kodi mungagwiritse ntchito bwanji bokosi limeneli? Muziwerenga mofatsa lemba lililonse limene lili m’bokosimo. Kenako werengani funso lomwe lili kutsogolo kwa lembalo. Ganizirani mozama yankho lake. Mukhozanso kufufuza mfundo zina. Komanso mungadzifunse mafunso ena ngati akuti, ‘Kodi zimenezi zikundiuza chiyani zokhudza Yehova? Kodi zikukhudza bwanji moyo wanga? Kodi ndingazigwiritse ntchito bwanji pothandiza ena?’

24 Kuganizira mwa njira imeneyi kungatithandize kuti tilimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Baibulo limati pali kugwirizana pakati pa zimene timaganiza ndi mtima wathu. (Salimo 19:14) Tikamaganizira moyamikira zimene timaphunzira zokhudza Mulungu, zimenezo zimakhazikika mumtima mwathu. Ndiyeno zimakhudza mmene timaganizira, mmene timamvera ndipo kenako zimatithandiza kuchitapo kanthu. Timayamba kukonda kwambiri Mulungu, ndipo chikondi chimenecho chimatichititsa kuti tizifuna kumusangalatsa ngati Mnzathu wapamtima. (1 Yohane 5:3) Kuti Yehova akhale Mnzathu wotero, tifunika kudziwa makhalidwe ake komanso mmene amachitira zinthu. Komabe, choyamba tiyeni tikambirane mfundo ina yokhudza Mulungu yomwenso imatithandiza kuti tizifunitsitsa kuti iye akhale mnzathu. Mfundo yake ndi yoti iye ndi woyera.

a Mwachitsanzo, Baibulo limanena za nkhope ya Mulungu, maso ake, makutu ake, mphuno yake, pakamwa pake, mkono wake ndi mapazi ake. (Salimo 18:15; 27:8; 44:3; Yesaya 60:13; Mateyu 4:4; 1 Petulo 3:12) Sitiyenera kuganiza kuti mawu ophiphiritsa amenewa akusonyeza kuti Yehova alidi ndi ziwalo zimenezi, monganso mmene zilili ndi mawu amene amanena kuti iye ndi “Thanthwe” kapena “chishango.”​—Deuteronomo 32:4; Salimo 84:11.